bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 26
Genesis 26
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 27 →
1
M'dzikomo mudaloŵanso njala kuwonjezera pa imene idaaloŵa pa nthaŵi ya Abrahamu. Ndipo Isaki adapita kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari.
2
Tsono Chauta adaonekera Isaki namuuza kuti, “Usapite ku Ejipito, koma ukhale m'dziko limene ndidzakuuza kuti ukhalemo.
3
Khala kuno ndipo Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakudalitsa chifukwa ndidzapereka maiko onseŵa kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako. Ndidzasunga lumbiro limene ndidachita kwa bambo wako Abrahamu.
4
Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka monga momwe ziliri nyenyezi zakuthambo, ndipo zidzukulu zakozo ndidzazipatsa maiko onseŵa. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa zidzukulu zako.
5
Ndidzakudalitsa iwe chifukwa Abrahamu adandimvera, ndipo adatsata malamulo ndi malangizo anga onse.”
6
Motero Isaki adakhala ku Gerari.
7
Anthu akumeneko atafunsa za mkazi wake, Isaki adati, “Ameneyu ndi mlongo wanga.” Ankachita mantha kunena kuti, “Ndi mkazi wanga.” Ankaopa kuti anthu akumenekowo angamuphe ndipo angakwatire Rebeka, popeza kuti anali wokongola kwambiri.
8
Isaki atakhala kumeneko kanthaŵi ndithu, Abimeleki mfumu ya Afilisti adasuzumira pa zenera kuyang'ana kunja, naona Isaki atakumbatira Rebeka.
9
Apo Abimeleki adatuma munthu kukaitana Isaki. Ndipo adati, “Ameneyu ndi mkazi wako ndithu. Bwanji mujamu unkanena kuti ndi mlongo wako?” Iye adayankha kuti, “Ndinkaganiza kuti ndidzaphedwa ndikanena kuti ndi mkazi wanga.”
10
Abimeleki adamufunsa kuti, “Bwanji iwe wachita zotere? Wina mwa anthu angaŵa bwenzi atamfunsira mkazi wako, iweyo ukadatichimwitsa.”
11
Tsono Abimeleki adalamula anthu ake onse kuti, “Musamuchite kanthu munthuyu pamodzi ndi mkazi wake yemwe. Wina aliyense akangotero, aphedwa.”
12
Isaki adabzala mbeu m'dzikomo, ndipo chaka chimenecho adakolola dzinthu dzochuluka koposa, chifukwa Chauta adaamudalitsa.
13
Chuma chake chidanka chichulukirachulukira, ndipo adasanduka munthu wolemera kwambiri.
14
Afilisti adayamba kuchita naye kaduka, chifukwa choti anali ndi nkhosa ndi ng'ombe zambiri, pamodzi ndi akapolo ochuluka.
15
(Anthuwo anali atakwirira zitsime zonse zimene antchito a bambo wake Abrahamu adaakumba, Abrahamuyo adakali ndi moyo.)
16
Tsono Abimeleki adauza Isaki kuti, “Muchoke kuno. Inu ndinu amphamvu kupambana ife.”
17
Motero Isaki adachoka nakamanga mahema m'chigwa cha Gerari nakhazikikako.
18
Kumeneko adafukulanso zitsime zimene anthu adaakumba pa nthaŵi ya Abrahamu bambo wake. Atafa Abrahamuyo, Afilisti adaazikwirira zitsimezo. Isaki adazitcha zitsimezo maina omwewo amene bambo wake ankazitchula.
19
Antchito a Isaki adakumba chitsime m'chigwa, napezamo madzi.
20
Koma abusa a ku Gerari adayamba kukangana ndi abusa a Isaki, ankati, “Madziŵa ndi athu.” Motero chitsimecho Isaki adachitcha Mkangano, chifukwa adakangana naye.
21
Antchito a Isaki aja adakumba chitsime china, ndipo padaukanso mkangano wina pa za chitsime chimenecho. Motero adachitcha Chidani.
22
Adachoka kumeneko, nakakumba chitsime china. Pa chimenechi panalibe mkangano, motero adachitcha Ufulu. Adati, “Tsopano Chauta watipatsa ufulu m'dziko, ndipo tidzalemera kuno.”
23
Patapita nthaŵi, Isaki adachoka napita ku Beereseba.
24
Usiku Chauta adamuwonekera namuuza kuti, “Ine ndine Mulungu wa bambo wako Abrahamu. Usachite mantha poti Ine ndili nawe. Ndidzakudalitsa, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri chifukwa cha mtumiki wanga Abrahamu.”
25
Tsono Isaki adamanga guwa kumeneko, natama dzina la Chauta mopemba, namanga hema lake komweko, ndipo antchito ake adakumba chitsime komweko.
26
Abimeleki adachoka ku Gerari nabwera kudzacheza ndi Isaki pamodzi ndi Ahuzati, nduna yake, ndi Fikolo mtsogoleri wa ankhondo.
27
Tsono Isaki adaŵafunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani mwabwera kuno kudzandiwona, pamene kale mudaandiwonetsa mtima woipa mpaka kundichotsa m'dziko mwanu?”
28
Iwowo adayankha kuti, “Tsopano tikudziŵa kuti Chauta ali nanu, ndipo taganiza zoti inu ndi ife tichite chipangano. Tikufuna kuti inu mulonjeze
29
kuti simudzatichita zoipa, monga ife sitidakuchiteni zoipa. Tidakuchitirani zabwino, ndipo tidakulolani kuti mupite mwamtendere. Tsopano Chauta wakudalitsani.”
30
Isaki adaŵakonzera phwando, ndipo anthuwo adadya ndi kumwa.
31
M'maŵa kutacha, munthu aliyense adalonjeza ndi kulumbira. Kenaka Isaki adaŵaperekeza, ndipo onsewo adachoka mwamtendere, napita.
32
Tsiku limenelo antchito ake a Isaki adabwera kudzamuuza za chitsime chimene iwowo adaakumba. Adati, “Tapeza madzi.”
33
Isaki adachitcha Siba. Nchifukwa chake mzindawo umatchedwa Beereseba mpaka lero lino.
34
Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, adakwatira Yuditi mwana wa Beeri Muhiti. Adakwatiranso Basemati, mwana wa Eloni Muhiti.
35
Onseŵa adapezetsa Isaki ndi Rebeka mavuto aakulu.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
Recommended Reading
Commentary
Genesis Commentaries
→
Devotional
Genesis Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→