bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 13
Genesis 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 14 →
1
Abramu ndi mkazi wake atachoka ku Ejipito, adapita ku Negebu, chigawo chakumwera. Ndipo Loti adapita nawo limodzi.
2
Abramu anali wolemera kwambiri. Anali ndi zoŵeta monga: nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe, ndiponso siliva ndi golide yemwe.
3
Kuchokera kumwera adasendera ndithu cha ku Betele, ku malo aja kumene kale adaamangako hema lake, pakati pa Betele ndi Ai.
4
Tsono adabwereranso ku malo aja kumene kale adaamangako guwa, ndipo adatama dzina la Chauta mopemba.
5
Loti nayenso amene ankayenda limodzi ndi Abramu, anali ndi nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe pamodzi ndi banja lake ndi antchito ake amene ankakhala naye limodzi.
6
Tsono dziko lodyetsapo zoŵeta linali losakwanira onse aŵiriwo, poti aliyense anali ndi zoŵeta zambiri.
7
Motero padaauka ndeu pakati pa abusa a Abramu ndi abusa a Loti. Nthaŵi imeneyo nkuti Akanani ndi Aperizi akadalipo m'dzikomo.
8
Tsono Abramu adauza Loti kuti, “Ifetu ndife abale, choncho pasakhale kukangana pakati pa iwe ndi ine, ndipo abusa ako sayenera kumakangana ndi abusa anga.
9
Tiye tisiyane, usankhe dera lina lililonse la dziko lino limene ufuna. Iwe ukapita kwina, inenso ndipita kwina.”
10
Motero Loti atayang'anayang'ana, adaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yordani mpaka ku Zowari chili ndi madzi ambiri. Chigwacho chinali ngati munda wa Chauta kapenanso ngati dziko la Ejipito. Nthaŵi imeneyi nkuti Chauta asanaononge mizinda ya Sodomu ndi Gomora.
11
Loti adadzisankhira chigwa chonse cha Yordani, napita kukakhala chakuvuma. Umu ndimo m'mene anthu aŵiriwo adasiyanirana.
12
Abramu adakhala m'dziko la Kanani, koma Loti adakhazikika pakati pa mizinda yam'chigwa, nakamanga hema pafupi ndi mzinda wa Sodomu.
13
Anthu amumzindawo anali oipa kwambiri, ndipo ankachimwira Chauta.
14
Loti atachoka, Chauta adauza Abramu kuti, “Uyang'ane bwino kumpoto, kumwera, kuvuma ndi kuzambwe.
15
Ndidzakupatsa dziko lonse limene ukuliwonalo, iweyo pamodzi ndi zidzukulu zako. Ndipo lidzakhala lako mpaka muyaya.
16
Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kudzaziŵerenga. Yekhayo amene angaŵerenge fumbi la pa dziko lapansi, ndiye adzathe kuŵerenga zidzukulu zakozo.
17
Nyamuka tsopano, uyendere dziko lonselo, chifukwa ndakupatsa,”
18
Motero Abramu adazula hema lake, nakakhala patsinde pa mitengo ya thundu ya ku Mamure, imene ili ku Hebroni. Ndipo kumeneko adamangira Chauta guwa.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50