bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 29
Genesis 29
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 30 →
1
Tsono Yakobe adapitirira ulendo wake, kupita ku dziko la anthu akuvuma.
2
Atafikako adaona chitsime ku busa, ndiponso magulu atatu a nkhosa zitagona pambali pa chitsimecho. Nkhosazo zinkamwa m'chitsime chimenechi chomwe pamwamba pake panali mwala waukulu.
3
Nkhosa zonsezo zitasonkhana pamodzi kumeneko, abusa oŵeta nkhosazo ndiwo ankachotsa mwalawo pachitsimepo, kuti nkhosa zaozo zimwe. Zitatha kumwako, ankakunkhunizanso mwalawo kutseka pachitsimepo.
4
Yakobe adaŵafunsa abusawo kuti, “Kodi abale anga mukuchokera kuti?” Iwowo adayankha kuti, “Tikuchokera ku Harani.”
5
Yakobe adafunsanso kuti, “Kodi Labani mwana wa Nahori mumamdziŵa?” Iwowo adayankha kuti, “Ee, timamdziŵa.”
6
Adaŵafunsanso kuti, “Kodi ali bwino?” Iwowo adayankha kuti, “Ee, ali bwino. Suuyu Rakele, mwana wake, akubwera ndi nkhosayu.”
7
Tsono Yakobe adati, “Popeza kuti kukali masana, ndipo nthaŵi yokazilonga sinakwane, bwanji osati muzimwetse madzi, muzitengenso kukazidyetsa?”
8
Iwo aja adayankha kuti, “Sitingathe kutero mpaka nkhosa zonse zitasonkhana pamodzi, ndipo mwala wa pamwamba pa chitsimewo titaukunkhuniza. Apo tingathe kuzipatsa madzi nkhosazo.”
9
Yakobe akulankhulabe ndi iwowo, Rakele adafika ndi nkhosa za atate ake. Iyeyo ndiye ankaŵeta nkhosazo.
10
Yakobe ataona Rakele ali ndi nkhosa za bambo wake Labani, adapita kuchitsimeko, nakunkhuniza mwalawo, nkuzimwetsa madzi nkhosa za Labanizo.
11
Tsono Yakobe adamumpsompsona Rakeleyo, nalira mokweza.
12
Ndipo adamuuza kuti, “Ine ndine mwana wa Rebeka, mlongo wa atate ako.” Pomwepo Rakele adathamanga kukauza atate ake.
13
Labani atamva za Yakobe mwana wa mlongo wake, adathamanga kukakumana naye. Adamkumbatira, namumpsompsona, nkupita naye kunyumba. Tsono Yakobe adafotokozera Labani zonse zimene zidachitika.
14
Apo Labani adamuuza kuti, “Inde, zoonadi, iwe ndiwe mbale wanga weniweni.” Yakobe adakhala kumeneko mwezi wathunthu.
15
Tsono Labani adauza Yakobe kuti, “Suyenera kundigwirira ntchito popanda malipiro, chifukwa choti ndife abale. Undiwuze zimene ukufuna kuti ndikulipire.”
16
Labani anali ndi ana aakazi aŵiri, wamkulu Leya, wamng'ono Rakele.
17
Leya anali ndi maso ofooka, koma Rakele anali chiphadzuŵa.
18
Yakobe ankakonda Rakele, ndipo adati, “Ndidzakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi ziŵiri chifukwa cha mwana wanu Rakele.”
19
Choncho Labani adati, “Ndi bwino kwambiri kuti Rakeleyu ndipatse iwe, osati munthu wina aliyense. Khala ndi ine.”
20
Motero Yakobe adagwira ntchito zaka zisanu ndi ziŵiri kuti akwatire Rakele, ndipo nthaŵi imeneyo idangooneka kwa iye ngati masiku oŵerengeka chabe, chifukwa choti adaamkonda kwambiri mkaziyo.
21
Yakobe adauza Labani kuti, “Tsopano nthaŵi yatha. Patseni mwana wanuyu kuti ndimkwatire.”
22
Motero Labani adakonza phwando laukwati, naitana anthu onse akumeneko.
23
Koma usiku umenewo Labani adatenga Leya m'malo mwa Rakele nampatsa Yakobe, ndipo Yakobe adaloŵana ndi Leya.
24
(Nthaŵi yomweyo Labani adaperekanso mdzakazi wake Zilipa kwa Leya.)
25
M'maŵa mwake kutacha, Yakobe adaona kuti mkaziyo ndi Leya. Tsono adafunsa Labani kuti, “Chifukwa chiyani mwandichita zotere? Kodi suja ndidakugwirirani ntchito kuti ndikwatire Rakele? Chifukwa chiyani tsono mwandinyenga?”
26
Labani adayankha kuti, “Si mwambo wathu kuno kukwatitsa wamng'ono, mkulu wake asanakwatiwe.
27
Dikira, yamba watsiriza mlungu uno wa chikondwerero chaukwati, kenaka ndidzakupatsa Rakele, komatu udzandigwiriranso ntchito zaka zina zisanu ndi ziŵiri.”
28
Yakobe adavomera, ndipo mlungu wa chikondwerero chaukwati utapita, Labani adapereka Rakele kwa Yakobe kuti akhale mkazi wake.
29
(Nthaŵi yomweyo Labani adaperekanso mdzakazi wake Biliha kwa Rakele.)
30
Motero Yakobe adaloŵana ndi Rakele, ndipo adamkonda kupambana Leya. Tsono adamgwiriranso ntchito Labani zaka zina zisanu ndi ziŵiri.
31
Chauta ataona kuti Yakobe sankakonda kwambiri Leya, adalola kuti Leyayo abale ana, koma Rakele ai.
32
Leya adatenga pathupi, ndipo adabala mwana wamwamuna. Tsono adati, “Chauta waona zovuta zanga. Ndithu tsopano mwamuna wanga adzayamba kundikonda.” Motero mwanayo adamutcha Rubeni.
33
Adatenganso pena pathupi, nabala mwana wina wamwamuna, ndipo adati, “Chauta wandipatsanso mwana wamwamunayu, chifukwa choti adamva kuti mwamuna wanga ine sandikonda.” Motero mwanayo adamutcha Simeoni.
34
Adatenganso pena pathupi, nabalanso mwana wina wamwamuna, ndipo adati, “Tsopano mwamuna wanga azindikonda kwambiri, popeza kuti ndamubalira ana aamuna atatu.” Motero mwanayo adamutcha Levi.
35
Adatenganso pena pathupi, nabala mwana winanso wamwamuna, ndipo adati, “Tsopano ndidzatamanda Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Yuda. Apo adayamba walekeza kubala.
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 30 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50