bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 23
Genesis 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 24 →
1
Sara adakhala ndi moyo zaka 127,
2
ndipo adafera ku Kiriyati-Ariba (ndiye kuti Hebroni) m'dziko la Kanani. Abrahamu adapita kumeneko nakalira maliro a Sarayo.
3
Kenaka adasiya mtembo wa mkazi wakewo, nakalankhula ndi anthu a ku Hiti kuti,
4
“Ine ndine mlendo kwanu kuno, wongoyenda. Mundigulitseko kadziko kuti kakhale manda, kuti ndiike mkazi wanga.”
5
Anthuwo adamuyankha kuti,
6
“Timvereni, mbuyathu. Inu ndinu nduna yaikulu pakati pathu pano. Mkazi wanuyu, mumuike m'manda aliwonse abwino amene tili nawo. Palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu pano amene angakumaneni manda amene tili nawo, kapena kukuletsani kuikamo amaiŵa.”
7
Apo Abrahamu adaimirira nkuŵeramira anthuwo,
8
naŵauza kuti, “Ngati mukuvomera kuti ndiike mkazi wangayu kuno, chonde pemphereni Efuroni Muhiti, mwana wa Zohari,
9
kuti andigulitse phanga la Makipera ali naloli. Phangalo lili m'malire a munda wake. Mpempheni kuti andigulitse pa mtengo wake ndithu, inu mukupenya, kuti malowo ndiŵasandutse manda.”
10
Pamenepo nkuti Efuroniyo ali pamodzi ndi Ahiti ku malo ochitirako msonkhano pa chipata cha mudzi. Ndipo anthu onsewo akumva, iye adayankha kuti,
11
“Ai, mbuyanga. Ine ndikupatsani munda wonsewu pamodzi ndi phanga lomweli. Ndikupatsani chabe malowo pamaso pa anthu anga onseŵa, kuti muikemo amai amene atisiyaŵa.”
12
Apo Abrahamu adaŵerama pamaso pa anthu onse aja,
13
nauza Efuroni pakhamu pa onse kuti, “Koma chonde, mundimvere, ine ndichita kugula mundawu. Landirani ndalama za mtengo wake wa mundawu, kuti mkazi wanga ndidzamuike m'menemo.”
14
Koma Efuroni adayankha kuti,
15
“Mvereni, mbuyanga. Malowo mtengo wake ndi masekeli a siliva okwana 400. Koma zimenezo nchiyani pakati pa inu ndi ine? Ikani maliro anu.”
16
Abrahamu adavomera, ndipo pamaso pa anthu onse a ku Hiti adaŵerenga masekeli a siliva okwana 400 amene Efuroni adaatchula, potsata ndalama zomwe anthu amalonda ankagwiritsa ntchito m'dzikomo pa nthaŵi imeneyo.
17
Umu ndimo m'mene kadziko kaja ka Efuroni ka ku Makipera, kuvuma kwa Mamure, kadasandukira ka Abrahamu. Panali munda ndi phanga lokhala m'malire mwa mundawo, pamodzi ndi mitengo yonse yam'mundamo mpaka kukalekeza ku malire ake.
18
Ahiti amene anali pamsonkhanopo adachitira umboni kuti dera lonselo ndi la Abrahamu.
19
Pambuyo pake Abrahamu adaika mkazi wake Sara m'phanga la munda wa ku Makipera kuvuma kwa Mamure, (ndiye kuti Hebroni), m'dziko la Kanani.
20
Motero mundawo pamodzi ndi manda omwewo amene kale adaali a Ahiti, malo onsewo adapatsidwa kwa Abrahamu, ndipo iye adaŵasandutsa manda.
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50