bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 7
Genesis 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 8 →
1
Chauta adauza Nowa kuti, “Loŵa m'chombo iwe pamodzi ndi banja lako. Iwe wekha ndakupeza kuti ndiwe wochita zondikondweretsa mu mbadwo uno.
2
Tsono tenga magulu asanu ndi aŵiri a nyama, ziŵiriziŵiri, yaimuna ndi yaikazi, zimene amaperekera nsembe, ndipo utengenso nyama ziŵiriziŵiri, yaimuna ndi yaikazi, zosaperekera nsembe.
3
Utengekonso mbalame ziŵiriziŵiri za mtundu uliwonse, magulu asanu ndi aŵiri. Uchite zimenezi pofuna kuti nyama ndi mbalame za mitundu yonse zisungidwe ndi moyo, ndipo kuti zidzaswanenso pa dziko lapansi.
4
Pakangopita masiku asanu ndi aŵiri, ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anai, usana ndi usiku, kuti zife zamoyo zonse zimene ndidazipanga.”
5
Ndipo Nowa adachita zonse zimene Mulungu adamlamula.
6
Nowa anali wa zaka 600 pamene chigumulacho chidafika pa dziko lapansi.
7
Iyeyo ndi mkazi wake ndi ana ake aamuna ndi akazi ao adaloŵa m'chombo, kuthaŵa chigumulacho.
8
Nyama zazimuna ndi zazikazi zimene anthu amaperekera nsembe, mbalame pamodzi ndi nyama zokwaŵa zomwe,
9
Nowa adaloŵa nazo m'chombo, monga Mulungu adaalamulira.
10
Patangopita masiku asanu ndi aŵiri, chigumula chidafika pa dziko lonse lapansi.
11
Pa 17, mwezi wachiŵiri, Nowa ali wa zaka 600, akasupe onse a madzi ambiri okhala pansi pa dziko adatumphuka, ndipo kuthambo kudatsekukanso, kuti madzi akhuthuke.
12
Choncho mvula idagwa pa dziko lapansi masiku makumi anai, usana ndi usiku.
13
Pa tsiku lomwelo, Nowa ndi mkazi wake, pamodzi ndi ana ake aamuna, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi akazi ao, adaloŵa m'chombomo.
14
Iwowo adaloŵa m'chombo pamodzi ndi mtundu uliwonse wa nyama zakuthengo, zoŵeta, nyama zokwaŵa ndi mbalame za mtundu uliwonse.
15
Nowa adaloŵa m'chombomo pamodzi ndi zamoyo zonse zazimuna ndi zazikazi,
16
monga Mulungu adaalamulira. Pomwepo Chauta adatseka pa khomo.
17
Chigumula chidagundika masiku makumi anai pa dziko lapansi. Madzi adayamba kukwera pa dziko lapansi, ndipo chombo chidayamba kuyandama.
18
Madziwo adanka nakwererakwerera, ndipo chombocho chidayandama pa madzi.
19
Kukwera kwa madzi kudapitirira ndithu mpaka kumiza ndi mapiri aatali omwe.
20
Tsono adakwererakwerera ndithu mpaka kubzola nsonga za mapiriwo mamita asanu ndi aŵiri.
21
Zamoyo zonse zokhala pa dziko lapansi zidafa, monga mbalame, zoŵeta, nyama zakuthengo, mtindiri wa tizilombo tosiyanasiyana, ndi anthu onse.
22
Zamoyo zonse za pa dziko lapansi zidafa.
23
Chauta adaononga zamoyo zonse za pa dziko: anthu, nyama, zokwaŵa ndi mbalame. Nowa yekha adapulumuka pamodzi ndi onse amene anali naye m'chombomo.
24
Madziwo adakhala osaphwa konse pa dziko lapansi masiku 150.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50