bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 8
Genesis 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 9 →
1
Tsono Mulungu adakumbukira Nowa pamodzi ndi nyama zonse zakuthengo ndi zoŵeta zimene zinali naye m'chombomo. Adalamula mphepo kuti iwombe pa dziko lapansi, pomwepo madzi adayamba kutsika.
2
Akasupe a madzi ambiri okhala pansi pa dziko pamodzi ndi zipata zakuthambo, adazitseka. Mvula adailetsa,
3
ndipo madzi adayamba kutsika pang'onopang'ono. Masiku 150 atapita, madziwo anali atatsika ndithu,
4
ndipo pa tsiku la 17, mwezi wachisanu ndi chiŵiri, chombocho chidakaima pamwamba pa phiri la Ararati.
5
Madziwo adanka natsikabe, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wakhumi, nsonga za mapiri zidayamba kuwoneka.
6
Patapita masiku makumi anai, Nowa adatsekula zenera,
7
natulutsa khwangwala. Khwangwalayo ankangouluka mu mlengalenga kudikira kuti madzi aphwe pa dziko lapansi.
8
Tsono Nowa adatulutsa nkhunda kuti ikaone ngati madzi aphwa.
9
Koma popeza kuti madzi anali akadalipobe pa dziko lonse, nkhundayo idabwerera, chifukwa idaasoŵa potera. Nowa adatambalitsa dzanja kunja, nailoŵetsanso m'chombo muja.
10
Atadikira masiku asanu ndi aŵiri ena, adaitulutsanso nkhunda ija m'chombo.
11
Madzulo idabwerako, ndipo Nowa adaona kuti kukamwa kwake kuli tsamba laliŵisi la mtengo wa olivi. Apo Nowa adadziŵa kuti madzi ayamba kuphwa.
12
Pambuyo pake Nowa atadikiranso masiku ena asanu ndi aŵiri, adaitulutsanso nkhunda ija, koma nkhundayo sidabwererenso.
13
Nowa ali wa zaka 601, pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, madzi adaphweratu pa dziko lapansi. Nowa adatsekula zenera la chombo chija nayang'ana kunja, nkuwona kuti pansi pauma,
14
Pa tsiku la 27 mwezi wachiŵiri, dziko lonse lapansi linali litauma kotheratu.
15
Mulungu adauza Nowa kuti,
16
“Iwe ndi mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi ao, tulukani m'chombomo.
17
Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwezo, mbalame, nyama ndi zokwaŵa, kuti ziswane ndi kubalalika pa dziko lonse lapansi.”
18
Motero Nowa adatuluka m'chombo, iye ndi mkazi wake ndiponso ana ake ndi akazi ao.
19
Nyama zonse, zokwaŵa zonse, mbalame zonse, ndi zina zonse zoyenda pansi pano zidatuluka m'chombomo m'magulumagulu potsata mitundu yake.
20
Pamenepo Nowa adamanga guwa kumangira Chauta. Adatengako mtundu uliwonse wa nyama ndi mbalame zimene anthu amaperekera nsembe, ndipo adazipha, napereka nsembe zopsereza paguwapo.
21
Chauta atamva fungo lokomalo, adati, “Sindidzatembereranso dziko chifukwa cha zochita za anthu, chifukwa ndikudziŵa maganizo a munthu kuti ndi oipa kuyambira ali mwana. Sindidzaononganso zamoyo zonse monga ndachitiramu.
22
“Nthaŵi zonse m'mene dziko lapansi lidzakhalire, padzakhala nyengo yobzala ndi nyengo yokolola. Padzakhala nyengo yachisanu ndi nyengo yotentha, nyengo yachilimwe ndi nyengo yadzinja, ndipo usana ndi usiku zidzakhalapo kosalekeza.”
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50