bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 25
Genesis 25
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 26 →
1
Abrahamu adakwatiranso mkazi wina dzina lake Ketura.
2
Ketura adamubalira Zimirani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa.
3
Yokisani adabereka Sheba ndi Dedani, ndipo ana a Dedani anali Aasuri, Aletusi ndi Aleumi.
4
Ana a Midiyani anali Efa, Efera, Hanoki, Abida ndi Elida. Onseŵa anali zidzukulu za Ketura.
5
Abrahamu adasiyira Isaki zonse zimene anali nazo.
6
Koma asanafe adaŵapatsako mphatso ana ake ena aja amene adaŵabereka mwa akazi ake enawo. Onsewo adaŵatumiza ku dziko lakuvuma kuti akakhale kumeneko, kuŵachotsa kwa mwana wake Isaki.
7
Abrahamu adakhala ndi moyo zaka 175.
8
Adamwalira ali nkhalamba yotheratu, atagonera zaka zochuluka.
9
Ana ake aja, Isaki ndi Ismaele, adamuika m'phanga lija la Makipera, m'munda umene kale udaali wa Efuroni mwana wa Zohari wa ku Hiti. Mundawo unali chakuvuma kwa Mamure.
10
Unali munda umene Abrahamu adaagula kwa Ahiti. Abrahamu ndi mkazi wake Sara adaikidwa kumeneko.
11
Atamwalira Abrahamu, Mulungu adadalitsa mwana wake Isaki amene ankakhala pafupi ndi chitsime cha Wamoyo-Wondipenya chija.
12
Nazi zidzukulu za Ismaele, mwana wa Abrahamu amene adamubalira Hagara, mdzakazi wa ku Ejipito uja.
13
Maina a ana a Ismaele ndi aŵa: woyamba anali Nebayoti, pambuyo pake adabereka Kedara, Adibeele, Mibisamu,
14
Misima, Duma, Masa,
15
Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema.
16
Ameneŵa ndiwo ana a Ismaele malinga ndi midzi yao ndiponso zigono zao. Anali mafumu khumi ndi aŵiri a mafuko osiyana.
17
(Ismaele anali wa zaka 137 pa nthaŵi imene ankamwalira, ndipo adaikidwa m'manda.)
18
Zidzukulu za Ismaeleyo zinkakhala m'dziko la pakati pa Havila ndi Suri, kuvuma kwa Ejipito, pa njira ya ku Asiriya. Zinkakhala molekana ndi zidzukulu zina za Abrahamu.
19
Nayi mbiri ya Isaki mwana wa Abrahamu: Abrahamu adabereka Isaki,
20
ndipo pamene Isaki adakwatira Rebeka mwana wa Betuele Mwaramu wa ku Mesopotamiya, nkuti ali wa zaka makumi anai. Mlongo wa Rebekayo anali Labani, Mwaramu.
21
Tsono poti mkazi wa Isaki anali wosabereka, Isakiyo adapempherera mkazi wake kwa Chauta. Chauta adamva pemphero lake, ndipo Rebeka adatenga pathupi.
22
Koma pamene ana aŵiriwo anayamba kulimbana m'mimba mwake, adati, “Ngati umu ndimo m'mene zikhalire zinthu, ndikhaliranji ndi moyo?” Ndipo adakafunsa Chauta kuti amuyankhe.
23
Chauta adamuuza kuti, “M'mimba mwako muli mitundu iŵiri ya anthu. Udzabereka mafuko a anthu olimbana: mwana wina adzakhala wamphamvu kupambana mnzake, wamkulu adzakhala wotumikira wamng'ono.”
24
Nthaŵi yakuti achire itakwana, Rebeka adabala mapasa.
25
Mwana woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala chaubweya. Motero adamutcha Esau.
26
Pobadwa mng'ono wake, dzanja lake linali litagwira chidendene cha Esau. Motero adamutcha Yakobe. Pamene ana ameneŵa ankabadwa, nkuti Isaki ali wa zaka 60.
27
Anyamatawo adakula ndithu, ndipo Esau adasanduka mlenje wodziŵa kusaka nyama, wokonda kuyendayenda. Koma Yakobe anali wachete, wokonda kukhala kunyumba.
28
Tsono Isaki ankakonda Esau chifukwa ankadya nyama imene Esauyo ankamupatsa akapha. Koma Rebeka ankakonda Yakobe.
29
Tsiku lina Yakobe adaphika nyemba zofiira, Esau nkubwera kuchokera kuthengo.
30
Anali ndi njala zedi, motero adauza Yakobe kuti, “Ine njala yandipha. Patseko nyemba zofiira waphikazi.” (Nchifukwa chake adamutcha Edomu.)
31
Koma Yakobe adayankha kuti, “Uyambe wandipatsa ukulu wako wauchisamba, ndiye ndikupatse zimenezi.”
32
Esau adati, “Chabwino, inetu ndili pafupi kufa. Kodi ukulu wangawo udzandipinduliranji?”
33
Yakobe adati, “Uyambe walumbira kuti ukulu wakowo wandipatsadi.” Apo Esau adalumbira, nagulitsa ukulu wake wauchisamba kwa Yakobe.
34
Apo Yakobe adapatsa Esau buledi pamodzi ndi nyemba zija, ndipo Esau adadya namwera, kenaka adanyamuka nkuchokapo. Motero Esauyo adanyoza ukulu wake wauchisamba.
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
Recommended Reading
Commentary
Genesis Commentaries
→
Devotional
Genesis Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→