bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 10
Genesis 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 11 →
1
Nayi mibadwo ya ana a Nowa: Semu, Hamu ndi Yafeti. Atatu ameneŵa adabereka ana ao chitatha chigumula chija.
2
Ana a Yafeti anali Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Meseki ndi Tirasi.
3
Ana a Gomeri anali Asikenazi, Rifati ndi Togarima.
4
Ana a Yavani anali Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Dodanimu.
5
Iwoŵa ndiwo anali makolo a onse amene ankakhala m'mbali mwa nyanja, ndi pa zilumba zam'nyanja. Ameneŵa ndiwo ana a Yafeti. Mafuko ao anali osiyanasiyana, ndipo ankakhala m'maiko osiyanasiyana. Fuko lililonse linkalankhula chilankhulo chakechake.
6
Ana a Hamu anali Kusi, Ejipito, Libia ndi Kanani.
7
Ana a Kusi anali Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana a Raama anali Sheba ndi Dedani.
8
Kusi adabereka Nimirodi. Nimirodi anali wankhondo woyamba wanyonga pa dziko lapansi.
9
Iyeyu analinso mlenje wamkulu pamaso pa Chauta. Nchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo chakuti, “Ndiwe mlenje wamkulu pamaso pa Chauta, ngati Nimirodi.”
10
Ankalamulira ku Babiloni, ku Ereki, ndi ku Akadi. Maufumu onseŵa anali m'dziko la Sinara.
11
Iyeyu adachoka ku Sinara nakakhala ku Asiriya, ndipo adakamanga mizinda ya Ninive, Rehobotiiri, Kala,
12
ndi mzinda wa Reseni umene uli pakati pa Ninive ndi mzinda waukulu uja wa Kala.
13
Ejipito ndi amene anali kholo la anthu a ku Ludi, Anamu, Lehabu, Nafutu,
14
Patirusi, Kasilu ndi Kafitori, makolo a Afilisti.
15
Kanani adabereka mwana wake wachisamba dzina lake Sidoni, ndipo adaberekanso Heti.
16
Ameneŵa adabereka Ayebusi, Aamori, Agirigasi.
17
Ahivi, Aariki, Asini,
18
Aaravadi, Azemari ndi Ahamati. Pambuyo pake mafuko a Akananiwo adabalalika ponseponse,
19
mpaka ku malire a Kanani. Malirewo adayambira ku Sidoni namaloŵa ku Gerari mpaka ku Gaza ndi kumaloŵanso ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.
20
Ameneŵa ndiwo ana a Hamu ndipo ankakhala m'mafuko osiyanasiyana, ndi m'maiko osiyanasiyana. Fuko lililonse linkalankhula chilankhulo chakechake.
21
Semu ndiye kholo la ana onse a Eberi, ndiponso ndiye mkulu wake wa Yafeti. Iyeyu anali ndi ana.
22
Ana a Semu anali Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
23
Ana a Aramu anali Uzi, Hulu, Getere ndi Masi.
24
Aripakisadi adabereka Sela, ndipo Sela adabereka Eberi.
25
Eberi anali ndi ana aŵiri. Wina anali Pelegi, chifukwa pa nthaŵi ya moyo wake, anthu onse a pa dziko lapansi anali ogaŵikana. Dzina la mbale wake linali Yokotani.
26
Yokotani adabereka Alimodadi, Selefi, Hazara-Maveti, Yera,
27
Hadoramu, Uzali, Dikila,
28
Obala, Abimaele, Sheba,
29
Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onseŵa anali ana a Yokotani.
30
Dziko limene ankakhalamo lidayambira ku Mesa kumaloŵa ku Sefari ku mapiri chakuvuma.
31
Ameneŵa ndiwo zidzukulu za Semu. Mafuko ao anali osiyanasiyana, ndipo ankakhalanso m'maiko osiyanasiyana. Fuko lililonse linkalankhula chilankhulo chakechake.
32
Onseŵa ndiwo mafuko a zidzukulu za Nowa potsata mibadwo yao ndi mitundu yao. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idatuluka mwa mafuko a Nowa ameneŵa, chitatha chigumula chija.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50