bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 45
Genesis 45
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 44
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 46 →
1
Pamenepo Yosefe sadathenso kudzigwira pamaso pa onse omtumikira aja. Adanena mokweza mau kuti, “Onse atuluke muno.” Motero panalibe ndi mmodzi yemwe wotsalira pamene Yosefe ankadziwulula kwa abale ake aja.
2
Adalira momveka kotero kuti Aejipito adamva ndithu, ndipo mbiri ya zimenezo idakafika mpaka kwa mfumu.
3
Yosefe adauza abale ake kuti, “Ine ndine Yosefe. Kodi bambo wanga akali moyo?” Koma abale akewo adadzazidwa ndi mantha, kotero kuti sadathenso nkumuyankha komwe.
4
Tsono Yosefe adaŵauza kuti, “Chonde senderani pafupi.” Onse atabwera pafupi, Yosefe adati, “Ine ndine mbale wanu uja Yosefe, amene mudamgulitsa ku Ejipito.
5
Koma tsopano musataye mtima kapena kuvutika, popeza kuti Mulungu mwiniwake ndiye amene adanditumiziratu kuno, kuti motero apulumutse moyo wanu.
6
Chaka chino ndi chaka chachiŵiri cha njala. Koma zakhalabe zaka zisanu, ndipo pa zaka zimenezi anthu sadzalima kapena kukolola.
7
Mulungu adanditumiziratu ine kuno kuti ndikupulumutseni, kuti choncho ziwoneke zidzukulu zanu zambiri.
8
Motero sindinu amene mudanditumiza kuno ai, koma Mulungu. Iye wandisandutsa nduna yaikulu ya Farao. Dziko lonse lino lili m'manja mwanga. Ejipito yense ndikulamulira ndine.
9
Tsopano fulumirani, bwererani kwa bambo wanga, mukamuuze kuti mwana wanu Yosefe akunena kuti, ‘Mulungu wandikuza mpaka kukhala wolamulira Ejipito yense, tsono bwerani kuno, musachedwe.
10
Mungathe kudzakhala kuno ku dziko la Goseni, kuti mukhale pafupi ndi ine. Mudzakhale kuno inuyo, ana anu, zidzukulu zanu, nkhosa zanu ndi mbuzi zomwe, ng'ombe zanu pamodzi ndi zonse zimene muli nazo.
11
Mukadzakhala ku Goseni, ine ndizidzakusamalani. Zaka za njala zikalipobe zisanu. Sindifuna kuti inu musauke pamodzi ndi banja lanu, ndi onse amene muli nawo.’
12
Tsono nonsenu ndi Benjamini, mng'ono wangayu, mungathe kuwona kuti ndinedi amene ndikulankhula nanu.
13
Muuzeni bambo wanga kuti ndili pa ulemerero waukulu ku Ejipito kuno. Mukamuuzenso bambo wanga zonse zimene mwaonazi ndipo fulumirani, mubwere naye kuno.”
14
Atatero adakumbatira Benjamini, mng'ono wake uja, nayambanso kulira. Benjamini nayenso adayamba kulira atangomkumbatira.
15
Pambuyo pake adaŵampsompsona abale ake onse aja akulira. Kenaka abale ake aja adayamba kucheza naye Yosefe.
16
Zitamveka kunyumba kwa Farao kuti abale a Yosefe abwera, Faraoyo ndi antchito ake onse adakondwa kwambiri.
17
Ndipo Farao adauza Yosefe kuti, “Uŵauze abale ako kuti asenzetse nyama zao katundu, ndipo abwerere ku Kanani.
18
Tsono kumeneko akatenge bambo wao ndi mabanja ao, ndipo adzabwere kwa ine kuno. Ndidzaŵapatsa dziko lachonde ku Ejipito kuno, ndipo azidzadya za m'dziko lino.
19
Uŵauze kuti atenge ngolo za kuno ku Ejipito, kuti akazi ao akakwerepo pamodzi ndi ana omwe. Ndithu akamtenge bambo wao akabwere kuno.
20
Asakade nkhaŵa kuti asiya katundu wao kumeneko, chifukwa dziko lokoma lachonde la ku Ejipito kuno lidzakhala lao.”
21
Tsono ana a Israele adachitadi zimenezo. Yosefe adaŵapatsa ngolo monga Farao adaalamulira, naŵapatsa phoso lapaulendo.
22
Adapatsanso aliyense zovala zachikondwerero, koma Benjamini adampatsa mashikeli asiliva okwana 300, ndi zovala zisanu zachikondwerero.
23
Bambo wake adamtumizira abulu khumi osenza zipatso zokoma za ku Ejipito, ndi abulu khumi osenza tirigu, buledi ndi zakudya zina za bambo wake zapaulendo.
24
Tsono adaŵauza abale akewo kuti azipita, ndipo ponyamukapo adanena kuti, “Musakangane pa njira.”
25
Tsono iwo adachoka ku Ejipito, kubwerera ku Kanani kwa bambo wao Yakobe.
26
Atafika, adauza bambo wao kuti, “Yosefe ujatu ali moyo! Ndiye wolamulira Ejipito yense!” Yakobe adachita ngati wakomoka, pakuti sadakhulupirire zonena zaozo.
27
Komabe iwo atamuuza zonse zimene Yosefe adaaŵauza, ndipo iye ataona ngolo zimene Yosefe adaatumiza kuti iye akwerepo popita ku Ejipito, Yakobe adayamba kutsitsimuka.
28
Tsono adati, “Basi chabwino, mwana wanga Yosefe akali moyo. Ndipita ndikamuwone ndisanafe.”
← Chapter 44
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 46 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50