bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 9
Genesis 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 10 →
1
Mulungu adadalitsa Nowa ndi ana ake omwe, nati “Mubale ana ambiri ndi kuchulukana, kuti mudzaze dziko lonse lapansi.
2
Zamoyo zonse za pa dziko lapansi pamodzi ndi mbalame zomwe, nyama zokwaŵa ndi zonse zam'nyanja zidzakuwopani. Zonsezi ndaziika kuti muzilamule.
3
Tsopano mungathe kudya nyama zonse, monga ndidakulolani kudya ndiwo zamasamba. Ndakupatsani zonsezi kuti zikhale chakudya chanu.
4
Koma pali chinthu chimodzi chokha chimene simuyenera kudya, ndicho nyama imene ikali ndi magazi. Ndaletsa poti magaziwo ndiwo moyo wake.
5
Aliyense wopha munthu, adzaphedwa. Nyama iliyonse yopha munthu, idzaphedwa. Munthu aliyense wopha mnzake, iyenso aphedwe.
6
“Aliyense wopha munthu, nayenso adzaphedwa, pakuti munthu adalengedwa muchifaniziro cha Mulungu.
7
Tsopano mubalane, kuti zidzukulu zanu zidzachulukane ndi kudzabalalika pa dziko lonse lapansi.”
8
Mulungu adauza Nowa ndi ana ake kuti,
9
“Tsopano ndikuchita nanu chipangano, pamodzi ndi zidzukulu zanu,
10
ndi zamoyo zonse, mbalame, zoŵeta, nyama zakuthengo, ndi zina zonse zimene zidatuluka nanu m'chombo.
11
Chipanganocho ndi ichi: ‘Ndikulonjeza kuti sindidzaononganso zamoyo zonse ndi chigumula. Ndithu chigumula sichidzaononganso dziko lapansi.’ ”
12
Ndipo Mulungu adati, “Nachi chizindikiro cha chipangano chamuyaya chimene ndikuchiika pakati pa Ine ndi inu ndi cholengedwa chilichonse chimene chili ndi inu.
13
Ndikuika utawaleza m'mitambo, ndipo udzakhala chizindikiro cha chipangano pakati pa Ine ndi dziko lapansi.
14
Nthaŵi zonse pakakhala mitambo mu mlengalenga, ndipo pakaoneka utawaleza m'mitambomo,
15
ndizidzakumbukira lonjezo langa limene ndidachita ndi inu ndi nyama zonse, kuti chigumula chisadzaonongenso zamoyo zonse.
16
Utawaleza ukamadzaoneka m'mitambo, Ine ndidzaupenya, ndipo ndizidzakumbukira chipangano chamuyaya cha pakati pa Ine ndi zamoyo zonse zokhala pa dziko lapansi.
17
Chimenechi ndi chizindikiro cha chipangano chimene ndachita ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi.”
18
Ana a Nowa omwe adatuluka m'chombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu ndiye anali bambo wa Kanani.
19
Ana a Nowa atatu ameneŵa ndiwo makolo a anthu a pa dziko lonse lapansi.
20
Nowa anali mlimi ndipo anali woyamba kulima munda wamphesa.
21
Tsiku lina atangomwa vinyo, adaledzera, ndipo adavula zovala zake zonse, nakagona ali maliseche m'hema mwake.
22
Hamu, bambo wake wa Kanani, ataona kuti Nowa bambo wake ali maliseche, adapita nakauza abale ake aŵiri aja.
23
Koma Semu ndi Yafeti adatenga chofunda nachiika kumbuyo kwao, atachinyamula pa mapewa. Tsono adayenda chafutambuyo nafunditsa bambo wao. Sadapenyeko kumene kunali bambo wao uja ndipo sadaone maliseche ake.
24
Nowa atadzuka, adamva zonse zimene mwana wake wamng'onoyo adaachita,
25
ndipo adati, “Atembereredwe Kanani! Adzakhala kapolo weniweni wa abale ake.” Popitiriza mau adati,
26
“Atamandike Chauta, Mulungu wa Semu, Kanani adzakhale kapolo wa Semuyo.
27
Mulungu amkuze Yafeti. Zidzukulu zake zidzagaŵane madalitso ndi zidzukulu za Semu. Kanani adzakhale kapolo wa Yafetiyo.”
28
Chitatha chigumulacho, Nowa adakhala ndi moyo zaka zina 350.
29
Adamwalira ali wa zaka 950.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50