bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 4
Genesis 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 5 →
1
Adamu adakhala ndi mkazi wake Heva ndipo mkaziyo adatenga pathupi. Tsono adabala mwana wamwamuna, ndipo adati, “Ndalandira mwana wamwamuna mwa chithandizo cha Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Kaini.
2
Pambuyo pake adabalanso Abele, mng'ono wa Kaini. Abele anali woŵeta nkhosa, koma Kaini anali mlimi.
3
Patapita nthaŵi, Kaini adatenga zipatso zina zakumunda, nazipereka kwa Chauta.
4
Abele nayenso adatenga ana oyamba kubadwa a nkhosa zake, naŵapereka ngati nsembe, pamodzi ndi mafuta ake omwe. Tsono Chauta adakondwera ndi Abele, nalandira nsembe yake.
5
Koma Kaini Chauta sadakondwere naye ndipo sadalandire chopereka chake. Chifukwa cha zimenezi, Kainiyo adakwiya kwambiri, kotero kuti nkhope yake inali yakugwa ndi yamasinya.
6
Apo Chauta adafunsa Kainiyo kuti, “Kodi wakwiyiranji chotere? Chifukwa chiyani nkhope yako yagwa?
7
Ukadachita zabwino, ndikadakondwera nawe. Koma chifukwa choti wachita zoipa, tchimo lakukhalirira pa khomo ngati chilombo cholusa. Likulakalaka kuti likugwire, koma iweyo uligonjetse tchimolo.”
8
Tsiku lina Kaini adauza mng'ono wake Abele kuti, “Tiye tikayende.” Atangopita kwa okha, Kaini adaukira mng'ono wakeyo namupha.
9
Tsono Chauta adafunsa Kainiyo kuti, “Kodi mng'ono wako Abele ali kuti?” Iye adayankha kuti, “Sindikudziŵa. Kodi ndi ntchito yanga kusamala mng'ono wangayo?”
10
Chauta adamufunsanso kuti, “Kodi wachita chiyani? Magazi a mng'ono wako akulira kwa Ine kuchokera m'nthaka.
11
Tsopano watembereredwa, sudzailimanso nthaka yomwe yamwa magazi a mng'ono wako, amene waŵakhetsa ndi manja ako.
12
Ukamalima mbeu, nthakayo sidzakubalira, ndipo udzakhala womangoyendayenda, wosoŵa pokhala penipeni pa dziko lapansi.”
13
Kaini adauza Chauta kuti, “Chilango chimenechi nchopitirira mphamvu zanga.
14
Tsopano mwandipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu. Ndidzakhala wothaŵathaŵa pa dziko lapansi, ndipo aliyense wondipeza adzandipha.”
15
Koma Chauta adamuyankha kuti, “Iyai, aliyense wopha iwe Kaini adzalangidwa, ndipo Ineyo ndidzamulipsira kasanunkaŵiri.” Motero Chauta adaika chizindikiro pa Kaini kuchenjeza aliyense kuti asamuphe Kainiyo.
16
Tsono Kaini adachoka pamaso pa Chauta nakakhala m'dziko lotchedwa Nodi, kuvuma kwa Edeni.
17
Kaini adakhala ndi mkazi wake, mkaziyo adatenga pathupi, nabala mwana dzina lake Enoki. Tsono Kaini adamanga mzinda, nautcha dzina la mwana wake Enoki.
18
Enoki adabereka mwana namutcha Iradi. Iradi adabereka Mehuyaele. Mahuyaele adabereka Metusaele amene adabereka Lameki.
19
Lameki adakwatira akazi aŵiri. Dzina la mkazi wake woyamba linali Ada, la mkazi wachiŵiri linali Zila.
20
Ada adabala Yabala, ndipo iyeyu ndiye kholo la onse oŵeta zoŵeta ndi okhala m'mahema.
21
Mbale wake anali Yubale, ndipo ndiye kholo la onse okhoza kuimba zeze ndi toliro.
22
Zila adabala Tubala-Kaini. Iyeyu ndiye kholo la onse ogwira ntchito yosula mkuŵa ndi zitsulo. Mlongo wa Tubala-Kainiyo anali Naama.
23
Tsono Lameki adauza akazi akewo kuti, “Iwe Ada ndi iwe Zila, mverani mau anga. Tcherani khutu mumve, inu akazi anga. Ine ndapha munthu chifukwa anandipweteka. Ndamuphadi mnyamatayo amene anandimenya.
24
Ngati wopha Kaini amlipsira kasanunkaŵiri, ndiye kuti wopha ine Lameki adzamlipsira kokwanira 77.”
25
Adamu adakhalanso ndi Heva mkazi wake, ndipo adatenga pathupi nabala mwana. Tsono Hevayo adati, “Mulungu wandipatsa mwana woloŵa m'malo mwa Abele uja amene adaphedwa ndi Kaini.” Mwanayo adamutcha Seti.
26
Seti adabereka mwana namutcha Enosi. Nthaŵi imeneyo anthu adayamba kutama dzina la Chauta mopemba.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50