bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 28
Genesis 28
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 29 →
1
Pamenepo Isaki adaitana Yakobe namdalitsa, ndipo adamlamula kuti, “Usakwatire mkazi wa kuno ku Kanani.
2
Konzeka, upite ku Mesopotamiya, kwao kwa Betuele, bambo wa mai wakoyu. Kumeneko ukakwatire mmodzi mwa ana aakazi a Labani, mlongo wa mai wako.
3
Mulungu Mphambe adalitse ukwati wako, ndipo akupatse ana ochuluka, kuti udzakhale gulu lalikulu la mitundu yambiri ya anthu.
4
Akudalitse iwe pamodzi ndi zidzukulu zako monga momwe adadalitsira Abrahamu, kuti lidzakhale lakodi dziko limene ukakhalemolo, dziko limene adapatsa Abrahamu.”
5
Atatero Isaki adatumiza Yakobe ku Mesopotamiya kwa Labani, mwana wa Betuele Mwaramu. Labani anali mlongo wa Rebeka mai wa Yakobe ndi Esau.
6
Esau adamva kuti Isaki wadalitsa Yakobe, ndipo kuti Yakobeyo watumizidwa ku Mesopotamiya kuti akakwatire kumeneko. Adamvanso kuti pomudalitsapo, adamlamula kuti asadzakwatire mkazi wa ku Kanani.
7
Adamva kuti Yakobe wamvera bambo wake ndi mai wake, ndipo kuti wapita ku Mesopotamiya.
8
Pamenepo Esau adadziŵa kuti bambo wake Isaki sankaŵakonda akazi a ku Kanani.
9
Motero adapita kwa Ismaele mwana wa Abrahamu, nakwatira Maharati mwana wa Ismaele, mlongo wa Nebayoti.
10
Yakobe adanyamuka ulendo kuchoka ku Beereseba, kupita ku Harani.
11
Atafika pamalo pena, adaima pamenepo chifukwa dzuŵa linali litaloŵa. Adagona pompo atatsamira mwala.
12
Ndipo adalota akuwona makwerero ochoka pansi mpaka kukafika kumwamba. Angelo a Mulungu ankatsika ndi kumakwera pa makwererowo.
13
Chauta adaimirira pambali pake namuuza kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wa Abrahamu ndi wa Isaki. Dziko ukugonapoli ndidzakupatsa iwe pamodzi ndi zidzukulu zako.
14
Zidzukulu zakozo zidzachuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi. Zidzabalalikira ku mbali zonse: kuzambwe, kuvuma, kumpoto ndi kumwera. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadalitsidwa kudzera mwa iwe ndi zidzukulu zako.
15
Ndili nawe, ndidzakutchinjiriza kulikonse kumene udzapite, ndipo ndidzakubwezanso ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zonse ndakuuzazi.”
16
Yakobe atadzuka adati, “Ndithudi Chauta ali pano, ndipo ine sindimadziŵa.”
17
Tsono adachita mantha, nanena kuti, “Hi, malo ano ndi oopsa! Zoonadi pano mpa nyumba ya Mulungu ndiponso khomo la kumwamba.”
18
Yakobeyo adadzuka m'maŵa kwambiri, natenga mwala uja adaatsamirawu, nauimiritsa kuti ukhale mwala wachikumbutso. Tsono adauthira mafuta mwalawo.
19
Ndipo malowo adaŵatchula Betele. Poyamba mudziwo unkatchedwa Luzi.
20
Pomwepo Yakobe adalumbira kwa Mulungu, adati, “Mukakhala nane ndi kunditchinjiriza pa ulendo wangawu, ndipo mukandipatsa chakudya ndi zovala,
21
ndi kundibwezera bwino kwathu kwa atate anga, mudzakhala Mulungu wanga.
22
Mwala wachikumbutso ndauimiritsawu udzakhala nyumba yanu, ndipo ine ndidzakupatsani gawo lachikhumi la zonse zimene mudzandipatse.”
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 29 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50