bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 32
Genesis 32
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 33 →
1
Yakobe adanyamuka ulendo wake, ndipo angelo a Mulungu adakumana naye.
2
Ataŵaona, adati, “Ili ndi gulu la ankhondo a Mulungu.” Motero malowo adaŵatcha Mahanaimu.
3
Tsono Yakobe adatuma amithenga ake kwa Esau mbale wake ku Seiri, ku dziko la Edomu.
4
Adaŵalangiza kuti akauze Esau kuti, “Ine Yakobe mtumiki wanu ndinkakhala kwa Labani, ndipo ndakhalitsako mpaka tsopano lino.
5
Ndili ndi ng'ombe, abulu, nkhosa ndi mbuzi ndiponso akapolo ndi adzakazi. Ndikutumiza mau ameneŵa kwa inu mbuyanga, kuti mundikomere mtima!”
6
Amithengawo atabwerera kwa Yakobe adati, “Tidapita kwa mbale wanu Esau, ndipo akubwera kudzakumana nanu. Ali ndi anthu 400 pamodzi.”
7
Apo Yakobe adachita mantha kwambiri ndi kutaya mtima. Motero anthu amene anali nawo adaŵagaŵa m'magulu aŵiri, pamodzi ndi nkhosa, mbuzi, ng'ombe ndiponso ngamira.
8
Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Esau akabwera, ndipo akachita nkhondo ndi gulu loyambali, gulu linalo lingathe kuthaŵa.”
9
Pamenepo Yakobe adayamba kupemphera. Adati, “Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa bambo wanga Isaki, mundimve ine! Inu Chauta mudandiwuza kuti, ‘Bwerera ku dziko lako, dziko la abale ako, ndidzasamala kuti zinthu zikuyendere bwino.’
10
Ine sindiyenera kulandira chifundo ndi chikhulupiriro chonse chimene mwandiwonetsa ine mtumiki wanu. Ndidaoloka Yordani ndilibe nkanthu komwe, koma ndodo yokha, koma tsopano ndabwerera ndi magulu aŵiri aŵa.
11
Ndapota nanu, pulumutseni ku mphamvu za mbale wanga Esau. Ndikuwopa kuti mwina akubwera kudzatithira nkhondo, ndipo tonsefe adzatiwononga pamodzi ndi akazi ndi ana omweŵa.
12
Kumbukirani lonjezo lanu lija lakuti, ‘Ndithu ndidzasamala kuti zinthu zikuyendere bwino, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri zosaŵerengeka. Zidzakhala zochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja.’ ”
13
Atagona kumeneko, pambuyo pake adasankhula mphatso izi pa chuma chonse chimene anali nacho:
14
mbuzi zazikazi 200 ndi atonde makumi aŵiri, nkhosa zazikazi 200 ndi zamphongo makumi aŵiri,
15
ngamira zamkaka makumi atatu pamodzi ndi ana ake, ng'ombe zazikazi makumi anai, ndi zazimuna khumi, ndi abulu aakazi makumi aŵiri ndi amphongo khumi.
16
Gulu lililonse la zoŵeta adalipatsa mnyamata wosamala, ndipo adaŵauza onsewo kuti, “Inu mutsogoleko, ndipo poyenda ndi magulu a zoŵeta, muzisiya mpata pakati pa gulu lililonse.”
17
Adauza mnyamata woyamba kuti, “Mbale wanga Esau akakumana nawe ndi kukufunsa kuti, ‘Kodi mbuyako ndani? Nanga ukupita kuti? Nanga zoŵeta zili patsogolo pakozi nza yani?’
18
Iwe ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za mtumiki wanu Yakobe, ndipo akuzitumiza kwa inu mbuyake, kuti zikhale mphatso. Yakobe mwiniwake ali m'mbuyo mwathumu.’ ”
19
Tsono adauzanso mnyamata wake wachiŵiri mau omwewo, ndi wachitatu, mpaka onse amene ankayenda motsogoza zoŵeta. Adaŵauza kuti, “Zimenezi ndizo mukauze Esau, mukakumana naye.
20
Muzikati, ‘Ndiponso mtumiki wanu Yakobe ali m'mbuyo mwathumu.’ ” Yakobe ankaganiza kuti, “Ndimtsitsa mtima ndi mphatso zimene ndamtumizirazi, ndipo ndikakumana naye, mwina adzandilandira bwino.”
21
Choncho mphatsozo zidatsogola, ndipo usiku umenewo Yakobe adagona kumahema konkuja.
22
Usiku womwewo Yakobe adadzuka natenga akazi ake aŵiri, ndi adzakazi ake aŵiri aja, pamodzi ndi ana ake khumi ndi mmodzi, naoloka mtsinje wa Yaboki padooko pake.
23
Ataŵaolotsa onse aja, adaolotsanso chuma chake chonse.
24
Iye adangotsala yekha. Tsono kudadza munthu wina amene adalimbana naye mpaka m'matandakucha.
25
Munthuyo ataona kuti sakuphulapo kanthu, adamenya Yakobe m'nyung'unyu, nyung'unyuyo nkuguluka polimbanapo.
26
Apo munthuyo adati, “Taye ndizipita, chifukwa kulikucha.” Koma Yakobe adayankha kuti, “Sindikulola kuti upite mpaka utandidalitsa.”
27
Munthuyo adamufunsa kuti, “Dzina lako ndiwe yani?” Yakobe adayankha kuti, “Dzina langa ndine Yakobe.”
28
Munthu uja adati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobe. Walimbana ndi Mulungu ndi anthu, ndipo wapambana. Motero dzina lako lidzakhala Israele.”
29
Pomwepo Yakobe adati, “Choncho nanunso tandiwuzani dzina lanu.” Koma munthuyo adati, “Chifukwa chiyani ukundifunsa dzina?” Ndipo pompo munthu uja adadalitsa Yakobe.
30
Yakobe adati, “Ndamuwona Mulungu maso ndi maso, ndipo ndili moyobe.” Tsono malowo adaŵatcha Penuwele.
31
Dzuŵa lidamtulukira Yakobe pamene ankachoka ku Penuwele, ndipo ankayenda chotsimphina chifukwa cha nyung'unyu ija.
32
Nchifukwa chake mpaka lero lino zidzukulu zonse za Israele sizidya nyama yapanyung'unyu, chifukwa ndi pa mtsempha wa panyung'unyu pomwe Yakobe adaamenyedwa.
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 33 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50