bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 11
Genesis 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 12 →
1
Poyambayamba anthu onse a pa dziko lapansi ankalankhula chilankhulo chimodzi, ndipo mau amene ankalankhulawo anali amodzi.
2
Atasamukira chakuvuma, adakafika ku chigwa ku dziko la Sinara kumene adakhazikika.
3
Tsono adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuzitentha.” Motero m'malo mwa miyala adatenga njerwa, namangira phula m'malo mwa matope.
4
Ndipo adati, “Tsopano tiyeni timange mzinda wathu, ndipo nsanja yake italike mpaka kukafika kumwamba. Tikatero tidzatchuka ndithu, ndipo sitidzamwazikanso pa dziko lapansi.”
5
Tsono Chauta adatsika kudzaona mzindawo, pamodzi ndi nsanja imene anthu ankamanga.
6
Ndipo adati, “Tsopano anthu onseŵa ndi amodzi, ndipo akulankhula chilankhulo chimodzi. Zinthu akuchitazi ndi chiyambi chabe cha zimene adzachite. Kenaka iwoŵa adzachita chilichonse chimene afuna.
7
Tiyeni titsikire komweko, tikasokoneze chilankhulo chao kuti asamvane.”
8
Motero Chauta adaŵamwaza anthuwo pa dziko lonse lapansi, ndipo iwowo adaleka kumanga mzindawo.
9
Choncho mzinda umenewo adautcha Babele, chifukwa choti kumeneko Chauta adasokoneza chilankhulo cha anthu onse. Ndipo kuchokera kumeneko adaŵamwaza anthuwo pa dziko lonse lapansi.
10
Nayi mibadwo yofumira mwa Semu: Patangopita zaka ziŵiri chitatha chigumula, Semu ali wa zaka 100, adabereka mwana dzina lake Aripakisadi.
11
Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 500, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
12
Pamene Aripakisadi anali wa zaka 35, adabereka mwana dzina lake Sela.
13
Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 403, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
14
Pamene Sela anali wa zaka 30, adabereka mwana dzina lake Eberi.
15
Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 403, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
16
Eberi ali wa zaka 34, adabereka mwana dzina lake Pelegi.
17
Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 430, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
18
Pelegi ali wa zaka 30 adabereka mwana dzina lake Reu.
19
Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 209, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
20
Reu ali wa zaka 32, adabereka mwana dzina lake Serugi.
21
Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 207, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
22
Serugi ali wa zaka 30, adabereka mwana dzina lake Nahori.
23
Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 200, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
24
Nahori ali wa zaka 29, adabereka mwana dzina lake Tera.
25
Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka 119, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
26
Tera ali wa zaka 70, adabereka Abramu, Nahori ndi Harani.
27
Nazi zidzukulu za Tera: Tera adabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Harani adabereka Loti.
28
Haraniyo adafera m'mudzi wa kwao dzina lake Uri, wa ku Kaldeya. Adafa atate ake akali moyo.
29
Abramu ndi Nahori adakwatira. Abramu adakwatira Sarai, ndipo Nahori adakwatira Milika mwana wa Harani, amene analinso bambo wake wa Isika.
30
Sarai analibe ana chifukwa anali wosabala.
31
Tsono Tera adatenga mwana wake Abramu ndi Loti mdzukulu wake, mwana wa Harani, ndiponso mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu. Adanyamuka ulendo kuchoka ku mzinda uja wa Uri wa ku Kaldeya napita nawo ku dziko la Kanani. Adakafika ku Harani, nakhazikika kumeneko.
32
Ndipo Tera adafera kumeneko ali wa zaka 205.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
Recommended Reading
Commentary
Genesis Commentaries
→
Devotional
Genesis Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→