bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 43
Genesis 43
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 42
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 44 →
1
Njala idakula kwambiri m'dziko la Kanani.
2
Tsono banja la Yakobe lija litadya tirigu yense amene adaakasuma ku Ejipito uja, Yakobe adauza ana ake aja kuti, “Pitaninso, mukatigulireko chakudya pang'ono.”
3
Apo Yuda adati, “Munthu uja adatichenjeza kolimba kuti sadzatilola kuwonekera pamaso pake, tikapanda kupita naye mng'ono wathuyu.
4
Mukatilola kuti timtenge, tipita kukakugulirani chakudya.
5
Mukapanda kulola, ife sitipita, popeza kuti munthu ameneyo adaneneratu kuti, ‘Sindidzakulolani kufika pamaso panga mukapanda kubwera naye mbale wanuyo.’ ”
6
Apo Israele adati, “Chifukwa chiyani mudathinitsa zinthu pa ine pomuuza kuti muli ndi mbale wanu winanso?”
7
Iwo adayankha kuti, “Ndiye kuti munthuyo ankangofunsitsa za ife ndi za banja lathu nkumati, ‘Kodi bambo wanu akali moyo? Kodi muli naye mbale wanu wina?’ Tsono ife tidaayenera kuyankha mafunso onseŵa. Nanga ife tikadadziŵa bwanji kuti iye atiwuza zoti mbale wathuyo tipite naye limodzi.”
8
Yuda adauza bambo wake Israele kuti, “Mnyamatayu patsani ine, ndipo tikonzeke kuti tinyamuke tizipita. Motero tonsefe, inuyo, ana athu pamodzi ndi ife, sitidzafa ndi njala.
9
Ine ndikhale ngati chikole cha moyo wake wa Benjamini. Ngati sindidzabwerera naye kuno ali moyo, inu mudzandiimbe mlandu moyo wanga wonse.
10
Tikadapanda kuzengereza, tikadapita ndi kubwerako kaŵiri konse tsopano.”
11
Tsono bambo wao Israele adaŵauza kuti, “Ngati ndi m'mene ziliri, chitani choncho. Munthuyo mtengereniko zipatso zokoma za dziko lino m'matumba mwanu kuti mukampatse. Mumtengerenso mafuta opaka pang'ono, uchi pang'ono, mafuta onunkhira osiyanasiyana, mure, mtedza, ndiponso zipatso zinanso.
12
Mutenge ndalama zokwanira, kuti mukabweze ndalama zomwe zidapezeka m'matumba mwanu zija. Makamaka zinthu zinali zitalakwika.
13
Mtengeni mbale wanuyu, ndipo nyamukani, mupitenso kwa munthuyo.
14
Mulungu Mphambe akuchitireni chifundo pamaso pa munthuyo, kuti abweze mbale wanu wina uja pamodzi ndi Benjamini. Ngati ana anga onse andifera, andifera ndithu basi.”
15
Motero abale onse aja adatenga mphatso zija, ndipo adatenganso ndalama moŵirikiza, namtenganso Benjamini. Tsono adakonzeka, nanyamuka ulendo kupita ku Ejipito. Kumeneko adakaonekera pamaso pa Yosefe.
16
Yosefe ataona Benjamini, adauza wantchito woyang'anira zonse panyumba pake kuti, “Anthu aŵa aloŵetse m'nyumba. Ndipo uphe nyama ndi kuiphika bwino, chifukwa anthu ameneŵa adya ndi ine masana ano.”
17
Wantchitoyo adachita monga momwe Yosefe adamuuzira, napita nawo abale aja kunyumba kwa Yosefe.
18
Koma iwowo adachita mantha kwambiri poona kuti akupita nawo kunyumba kwa Yosefeyo: ankaganiza kuti, “Akutiloŵetsa muno chifukwa cha ndalama zija zidabwezedwa m'matumba mwathu pa nthaŵi yoyamba ija. Akungofuna danga loti achite nafe nkhondo mwadzidzidzi, chifukwa akufuna kutisandutsa akapolo ake ndi kutilanda abulu athuŵa.”
19
Motero asanaloŵe m'nyumbamo adafika kwa wantchito wa Yosefe woyang'anira nyumba uja,
20
namuuza kuti, “Pepani bwana, ife tidaabweranso kuno kale kudzagula chakudya.
21
Titafika pa malo a chigono, pomasula matumba athu, aliyense mwa ife adapeza ndalama zake kukamwa kwa thumba lake, ndipo ndalamazo zinalipo zonse monga momwe tidaaŵerengera. Ndalama zimenezo tabwera nazo.
22
Ndipo tabwera nazonso ndalama zina zodzagulira chakudya china. Amene adaika ndalama m'matumba mwathu, sitikumudziŵa ai.”
23
Wantchito uja adati, “Musade nkhaŵa, mitima yanu ikhale pansi. Mulungu wanu, Mulungu wa atate anu, ndiye amene adakuikirani ndalama zanu m'matumbamo. Ndalama zanu zoyamba zija ndidalandira.” Atatero, adaŵatulutsira Simeoni uja.
24
Wantchitoyo atabwera nawo abalewo m'nyumba mwa Yosefe, adaŵapatsa madzi kuti asambe mapazi ao, ndipo abulu ao aja adaŵadyetsanso.
25
Tsono abalewo adakonzeratu mphatso zao zija kuti apereke kwa Yosefe masana, chifukwa anali atamva kuti akadya kumeneko.
26
Yosefe atabwera, abale akewo adapereka mphatso zija kwa iye, ndipo adamuweramira.
27
Iye adaŵafunsa m'mene aliri, naŵafunsanso kuti, “Kodi bambo wanu wokalamba uja munkandiwuzayu ali bwanji? Kodi akali moyo?”
28
Iwowo adayankha kuti, “Mtumiki wanu akali moyo, ndipo ali bwino.” Tsono onsewo adamgwadiranso namuŵeramira pomwepo.
29
Yosefe ataona Benjamini, mng'ono wake weniweni uja, adati “Uyu ayenera kukhala mng'ono wanu wotsiriza uja munkandiwuzayu. Mulungu akudalitse, mwana wanga.”
30
Atanena zimenezo Yosefe adachokapo mofulumira chifukwa choti mtima wake udaadzaza ndi chifundo chifukwa cha mng'ono wake uja. Anali pafupifupi kulira, motero adapita m'chipinda mwake nakalirira m'menemo.
31
Atapukuta m'maso adatuluka, ndipo adalimbanso mtima, nalamula kuti chakudya chibwere.
32
Yosefe ankadyera payekha, abale akewo ankadyera pa tebulo lina. Aejipito amene anali naye m'nyumba nawonso ankadyera paokha, chifukwa iwo ankanyansidwa kudyera pamodzi ndi Ahebri.
33
Abalewo adaakhala pa tebulo patsogolo pa Yosefe, ndipo anali ataŵaika motsatana ndi kubadwa kwao, kuyambira wamkulu mpaka wamng'ono. Abale aja ataona m'mene aŵakhazikira, adadabwa kwambiri namapenyetsetsana.
34
Chakudya chomwe ankadyacho chinkachokera patebulo pa Yosefe, koma chakudya chopatsa Benjamini chinkaposa cha onsewo kasanu. Motero onsewo adadya ndi kumwa pamodzi ndi Yosefe mpaka kukhuta, ndipo adasangalala pamodzi naye.
← Chapter 42
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 44 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50