bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 2
Genesis 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 3 →
1
Motero dziko lonse lapansi, thambo ndi zonse zokhala m'menemo, zidatha kulengedwa.
2
Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi Mulungu adamaliza ntchito imene ankachitayo, ndipo adapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri.
3
Mulungu adadalitsa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, naliyeretsa, chifukwa choti pa tsiku limenelo adapuma atatsiriza zonse zimene ankachita.
4
Ndimo m'mene dziko lapansi ndi zonse zakuthambo zidalengedwera. Pamene Chauta ankalenga dziko lapansi ndi zonse zakuthambo,
5
panalibe chomera chilichonse pa dziko lapansi, ndipo mbeu zinali zisanamere, chifukwa Chauta Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Ndipo panalibenso wina aliyense wolima pa nthaka.
6
Koma madzi ankatuluka m'dziko lonse lapansi ndi kumathirira nthaka.
7
Tsono Chauta adatenga dothi pa nthaka, ndipo adaumba munthu ndi dothilo. Adamuuzira mpweya wopatsa moyo m'mphuno zake, ndipo munthuyo adakhala wamoyo.
8
Kenaka Chauta adatsekula munda mu Edeni chakuvuma, ndipo munthu adamuumbayo adamkhazika m'menemo.
9
Chauta adameretsamo mitengo yokongola ya zipatso zokoma. Pakati pa mundawo panali mtengo wopatsa moyo, ndiponso mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa.
10
Mtsinje wotuluka mu Edeni momwemo, unkayenda numathirira mundawo. Mtsinjewo udagaŵika panai, nusanduka mitsinje inai.
11
Mtsinje woyamba ndi Pisoni, ndipo umayenda mozungulira dziko la Havila, kumene kumapezeka golide.
12
(Golide wakumeneko ndi wabwino. Kumapezekanso bedeliyo ndi miyala ya mtengowapatali yotchedwa onikisi.)
13
Mtsinje wachiŵiri ndi Gihoni, ndipo umayenda mozungulira dziko la Kusi.
14
Mtsinje wachitatu ndi Tigrisi, umene umayenda kuvuma kwa Asiriya. Mtsinje wachinai ndi Yufurate.
15
Tsono Chauta adamtenga munthuyo, namukhazika m'munda wa Edeni uja kuti azilima ndi kumausamala.
16
Ndipo Chauta adamlamula munthuyo kuti, “Uzidya zipatso za mtengo uliwonse wam'mundawu,
17
kupatula mtengo wokhawo umene umadziŵitsa zabwino ndi zoipa. Zipatso za mtengo umenewo usadye. Ukadzadya, ndithu udzafa!”
18
Pambuyo pake Chauta adati, “Sibwino kuti munthuyu akhale yekha. Ndipanga mnzake woti azimthandiza.”
19
Chauta adatenga dothi naumba nyama zonse ndi mbalame zonse, nabwera nazo kwa Adamu kuti azitche maina. Mwakuti maina amene Adamu adazitcha, maina ake ndi omwewo.
20
Adamu adazitcha maina nyama zonse, mbalame ndi zamoyo zonse zakuthengo. Komabe panalibe mnzake woti azimthandiza.
21
Tsono Chauta adagonetsa Adamu tulo tofanato, ndipo ali m'tulo choncho, Mulungu adamchotsako nthiti, natsekapo ndi mnofu pamalopo.
22
Chauta Mulungu adapanga mkazi ndi nthiti imene adaichotsa kwa Adamu uja, ndipo mkaziyo Mulungu adabwera naye kwa iye.
23
Adamu adati, “Uyutu ndiye ndi fupa lochokera ku mafupa anga, mnofu wochokera ku mnofu wanga. Adzatchedwa Mkazi, chifukwa watengedwa kwa Mwamuna.”
24
Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho aŵiriwo amakhala thupi limodzi.
25
Mwamunayo ndi mkazi wake uja, onse anali maliseche, komabe sankachita manyazi.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50