bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 35
Genesis 35
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 36 →
1
Tsono Mulungu adauza Yakobe kuti, “Nyamuka, pita ku Betele, ukakhale komweko. Ukamangeko guwa la Mulungu amene adakuwonekera pamene unkathaŵa mbale wako Esau.”
2
Motero Yakobe adauza banja lake ndi onse amene anali naye kuti, “Tayani milungu yachilendo imene muli nayo pakati panu. Mudziyeretse, ndipo muvale zovala zaudongo.
3
Tichokako kuno, tipita ku Betele kumene ndikamange guwa la Mulungu amene adandithandiza pa nthaŵi ya mavuto anga. Ndiye ndithu amene wakhala nane kulikonse komwe ndinkapita.”
4
Motero milungu yonse yachilendo imene ana ake anali nayo, adaipereka kwa Yakobe, pamodzinso ndi ndolo zakukhutu zimene ankavala. Zonsezo adazifotsera patsinde pa mtengo wa thundu pafupi ndi Sekemu.
5
Pamene Yakobe ndi ana ake adachoka, anthu onse a mizinda yozungulira adachita mantha, motero sadaŵatsatire.
6
Tsono Yakobe adafika ndi anthu ake ku Luzi (ndiye kuti Betele) m'dziko la Kanani.
7
Adamanga guwa kumeneko, ndipo malowo adaŵatcha Betele, chifukwa kumeneko nkumene Mulungu adadziwulula kwa Yakobe pamene ankathaŵa mbale wake.
8
Debora mlezi wa Rakele, adamwalira komweko, ndipo adaikidwa patsinde pa mtengo wathundu ku Beteleko. Motero malowo adatchedwa Mtengo Wamaliro.
9
Yakobe atabwerako ku Mesopotamiya kuja, Mulungu adamuwonekeranso namudalitsa.
10
Mulungu adati, “Dzina lako ndiwe Yakobe, koma kuyambira tsopano, dzina lako lidzakhala Israele.” Motero adayamba kutchedwa Israele.
11
Pambuyo pake Mulungu adamuuza kuti, “Ine ndine Mulungu, Mphambe. Ubale ana ambiri. Udzakhala ndi zidzukulu zambiri, ndipo zina mwa izo zidzakhala mafumu. Zidzukulu zako zidzachuluka kwambiri, kotero kuti zidzakhala mitundu yambiri ya anthu.
12
Ndidzakupatsa dziko limene ndidapatsa Abrahamu ndi Isaki. Dziko limeneli ndidzapatsanso zidzukulu zako, iwe utafa.”
13
Tsono Mulungu adamsiya Yakobe pa malo omwe ankalankhula nayepo, napita.
14
Yakobe adaimika chimwala chachikumbutso pa malo amenewo. Adapereka chopereka cha chakumwa pamwalapo, nathirapo mafuta.
15
Malo amene Mulungu adalankhula naye, Yakobe adaŵatcha Betele.
16
Tsono onse adachoka ku Betele, koma asanafike ku Efurata, nthaŵi yoti Rakele aone mwana idamukwanira, ndipo kubereka kwake kudamuvuta kwambiri.
17
Zidafika poipa kwambiri, ndipo mzamba adamuuza kuti, “Musaope, ameneyu ndi mwana wina wamwamuna.”
18
Tsono Rakele akumwalira kumene, akupuma mwaŵefuŵefu, kutsirizika, adamutcha mwanayo Benoni, koma bambo wake adamutcha Benjamini.
19
Rakele atamwalira, adaikidwa pambali pa mseu wopita ku Efurata (ndiye kuti Betelehemu.)
20
Ndipo Yakobe adaimika chimwala chachikumbutso pa manda a Rakele. Mwalawo ulipobe pamenepo mpaka lero lino.
21
Yakobe adapitirira nakamanga mahema ake kuseri kwa nsanja ya Edere.
22
Pamene Yakobe ankakhala m'dziko limenelo, Rubeni adaachita zoipa ndi Biliha, mmodzi wa azikazi a bambo wake, Yakobeyo nkuzimva zimenezo. Yakobe anali ndi ana aamuna khumi ndi aŵiri.
23
Ana a Leya anali aŵa: Rubeni, mwana wachisamba wa Yakobe, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara ndi Zebuloni.
24
Ana a Rakele anali aŵa: Yosefe ndi Benjamini.
25
Ana a Biliha mdzakazi wa Rakele anali aŵa: Dani ndi Nafutali.
26
Ana a Zilipa mdzakazi wa Leya anali aŵa: Gadi ndi Asere. Ameneŵa ndiwo ana a Yakobe amene adabadwira ku Mesopotamiya.
27
Yakobe adakafika kwa bambo wake Isaki ku Mamure (kumenenso kunkatchedwa ku Kiriyati-Ariba kapena Hebroni), kumene Abrahamu ndi Isaki ankakhala kale.
28
Tsono Isaki adamwalira ali wa zaka 180.
29
Ndipo adafa ndi kuikidwa m'manda, ali nkhalamba zedi. Ana ake, Esau ndi a Yakobe ndiwo adamuika m'manda.
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 36 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50