bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 42
Genesis 42
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 41
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 43 →
1
Yakobe atamva kuti ku Ejipito ndiko kuli tirigu, adafunsa ana ake kuti, “Chifukwa chiyani mukungokhala osachitapo kanthu?
2
Ndikumva kuti ku Ejipito aliko tirigu. Pitaniko kumeneko, mukatigulireko ife, kuti tingafe ndi njala.”
3
Motero abale ake a Yosefe khumi adanyamuka kupita ku Ejipito kukagula tirigu.
4
Yakobe sadamtume nawo Benjamini, mng'ono wake weniweni wa Yosefe uja, chifukwa ankaopa kuti angapeze tsoka.
5
Ana a Israelewo adapita ku Ejipito kukagula chakudya pamodzi ndi anthu ena onse, chifukwa chakuti ku dziko la Kanani kunali njala.
6
Tsono popeza kuti Yosefe anali nduna yaikulu yolamulira dziko lonse la Ejipito, ndiye amene ankagulitsa tirigu kwa anthu ochokera ku mbali zonse za dziko. Choncho abale ake a Yosefe nawonso adabwera, ndipo adamgwadira Yosefeyo, namuŵeramira.
7
Yosefe ataŵaona abale akewo, adaŵazindikira, koma adangochita ngati sadaŵadziŵe. Adayamba kuŵalankhula mozaza, naŵafunsa kuti, “Kodi inu mukuchokera kuti?” Iwo adayankha kuti, “Tikuchokera ku Kanani, tadzagula chakudya kuno.”
8
Yosefe adaŵazindikira abale ake aja, koma iwo sadamzindikire.
9
Adakumbukira maloto aja onena za iwo, ndipo adati, “Ndinu anthu ozonda dziko. Mwabwera kuno kudzazonda kuti muwone ngati dziko lathu ndi lofooka.”
10
Iwo aja adayankha kuti, “Iyai mbuyathu, ife atumiki anu tabwera kuti tidzagule chakudya basi.
11
Tonsefe tili pachibale. Sindife azondi, mbuyathu, koma ndife anthu okhulupirika ndithu.”
12
Yosefe adati, “Iyai. Inu mwabwera kudzazonda dziko lathu kuti muwone ngati ndi lofooka.”
13
Tsono iwowo adati, “Mbuyathu, ife tinalipo ana aamuna khumi ndi aŵiri pachibale pathu, bambo wathu mmodzi, ku dziko la kwathu ku Kanani. Wamng'ono ali ndi bambo wathu, ndipo wina adamwalira.”
14
Koma Yosefe adaŵayankha kuti, “Paja ndanena kale kuti ndinu azondi basi.
15
Tsono ndikuyesani motere; ndikulumbira kuti pali Farao! Inuyo simuchoka, mpaka mng'ono wanuyo atabwera kuno.
16
Tumani mmodzi mwa inu kuti apite akamtenge. Ena nonse otsalanu mukhale m'ndende ndithu, mpaka mau anuŵa atsimikizike, tiwone ngati mukunena zoona. Apo ai, ndithu pali Farao, inuyo ndinu azondi basi.”
17
Atanena mau ameneŵa, adakaŵatsekera m'ndende masiku atatu.
18
Patapita masiku atatu, adaŵauza kuti, “Ine ndimaopa Mulungu. Choncho ndikupatsani mwai woupulumutsa moyo wanu mukachita izi.
19
Ngati ndinu okhulupirika, mmodzi yekha atsalire m'ndendemu, ena nonsenu mungathe kupita, kuti mukapereke tirigu mwagulayu ku banja la kwanu kuli njalako.
20
Mng'ono wanuyo mukabwere naye kuno, kutsimikiza kuti mukunenadi zoona, ndipo simudzaphedwa.” Iwo aja adavomereza zimenezo.
21
Ndipo adayamba kuuzana kuti, “Ndithu, ife tidalakwa pamene mng'ono wathu ankatipempha kuti timchitire chifundo, koma ife osamumvera konse chifundo. Nchifukwa chake tili m'mavuto tsopano lino.”
22
Apo Rubeni adati, “Ine paja ndinkakuuzani kuti mnyamatuyu musamchite kanthu, inu osandimvera. Mwaonatu, tsopano tikulandira malipiro a imfa yake ija.”
23
Yosefe anali kumva zonse zimene ankakambiranazo, koma iwowo sadadziŵe, chifukwa choti ankalankhula naye kudzera mwa womasulira.
24
Tsono Yosefe adapita payekha kukalira misozi. Kenaka adabwerako nayambanso kulankhula nawo. Adapatulapo Simeoni, nammanga pomwepo iwowo akuwona.
25
Tsono Yosefe adalamula kuti matumba ao adzazidwe ndi tirigu, ndipo kuti ndalama za aliyense ziikidwe m'thumba mwake momwemo. Adalamulanso kuti aŵapatse kamba wapaulendo. Antchito a Yosefe adachitadi zonsezo.
26
Abale akewo adasenzetsa abulu ao matumba a tirigu uja adagulayu, ndipo adanyamuka ulendo.
27
Atafika pa chigono, mmodzi mwa iwo adamasula thumba lake kuti atengeko chakudya chodyetsa bulu wake. Atamasula, adangoona kuti pakamwa pa thumbalo pali ndalama.
28
Adaitana abale ake naŵauza kuti, “Ha, wandibwezera ndalama zanga. Si izi zili m'thumbazi.” Pamenepo onsewo mitima yao idangoti phwii! Adachita mantha kwambiri nati, “Mulungu watichita zotani ife?”
29
Atafika kwa bambo wao Yakobe, adamsimbira zonse zimene zidaŵagwera, adati,
30
“Nduna yaikulu ya dzikolo idatilankhula mozaza, kuti ati ndife ozonda dziko laolo.
31
Ife tidamuuza munthuyo kuti, ‘Ndife anthu okhulupirika, osati azondi.
32
Ife tonse tinalipo ana aamuna khumi ndi aŵiri, koma mmodzi adamwalira, ndipo wamng'ono ali ndi bambo wathu ku Kanani.’
33
Pamenepo iyeyo adati, ‘Kuti ndidziŵe kuti ndinu anthu okhulupirika, mmodzi mwa inu atsale ndi ine kuno, koma ena nonsenu mutenge tirigu, mupite naye ku banja la kwanu kuli njalako.
34
Ndipo mbale wanu wamng'onoyo mudzabwere naye kuno. Pamenepo ndiye ndidzadziŵe kuti sindinu azondi, koma ndinu okhulupirika. Mbale wanuyo ndidzambwezera kwa inu. Mukadzatero mungathe kumadzachitabe malonda m'dziko muno.’ ”
35
Atamasula matumba ao, aliyense adapeza kuti chikwama cha ndalama chinali momwe m'thumbamo. Ataona ndalamazo, iwowo pamodzi ndi bambo wao yemweyo adachita mantha kwambiri.
36
Tsono Yakobe bambo wao adaŵauza kuti, “Mwandilanda ana anga. Yosefe adapita, ndipo nayenso Simeoni wapita, tsopano mufuna kutenganso Benjamini, zonse zandigwera ine!”
37
Rubeni adauza atate ake kuti, “Mungathe kudzapha ana anga aŵiri, ngati Benjamini sindidzabwera naye kwa inu. Mundipatse kuti ndimsamale ndine, ndipo ndidzabwera naye.”
38
Koma Yakobe adati, “Mwana wangayu sangapite nanu ai, paja mbale wake adamwalira, ndipo ndi yekhayu watsala. Mwina mwake angathe kuphedwa pa njira, ndipo ine m'mene ndakalambiramu, chisoni chotere chidzangonditsiriza.”
← Chapter 41
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 43 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
Recommended Reading
Commentary
Genesis Commentaries
→
Devotional
Genesis Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→