bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 47
Genesis 47
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 46
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 48 →
1
Tsono Yosefe adatenga abale ake asanu napita nawo kwa Farao kukamuuza kuti, “Bambo wanga pamodzi ndi abale anga abwera kuchokera ku Kanani. Abwera ndi zoŵeta zao monga nkhosa ndi ng'ombe, pamodzi ndi zao zonse. Tsopano akukhala m'dziko la Goseni.”
2
Aŵa ndi asanu mwa abale angawo.
3
Apo Farao adaŵafunsa kuti, “Kodi mumagwira ntchito yanji?” Iwo adayankha kuti, “Ndife abusa bwana, monga momwe ankachitira makolo athu.”
4
“Tabwera kudzakhala nao m'dziko muno bwana, chifukwa ku Kanani kuli njala yoopsa, kotero kuti kulibe ndi msipu womwe wodyetsa zoŵeta. Chonde bwana, mutilole tikakhale ku dziko la Goseni.”
5
Tsono Farao adauza Yosefe kuti, “Bambo wako pamodzi ndi abale ako abwera kwa iwe.
6
Dziko la Ejipito lili m'manja mwako. Ukhazike bambo wako pamodzi ndi abale ako m'dziko lachonde, akakhale ku Goseni. Ndipo ngati ena mwa iwo ndi akatswiri a zoŵeta, uŵapatse ukapitao woyang'anira zoŵeta zanga.”
7
Yosefe adatenga bambo wake Yakobe, napita naye kwa Farao. Ndipo Yakobe adadalitsa Faraoyo.
8
Kenaka Farao adafunsa Yakobe kuti, “Muli ndi zaka zingati?”
9
Yakobe adayankha kuti, “Zaka za maulendo anga zakwana 130. Zaka zimenezi nzochepa ndiponso zamavuto, zosalingana ndi zaka za makolo anga pa nthaŵi yao yonse pamene anali moyo.”
10
Ndipo atadalitsa Farao, adatsazikana naye nkuchokapo.
11
Yosefe adamkhazika m'dziko la Ejipito bambo wake uja, pamodzi ndi abale ake onse aja, ndipo adaŵapatsa malo a nthaka yabwino ndi yachonde, m'chigawo chotchedwa Ramsesi, monga momwe Farao adaalamulira.
12
Yosefe adapereka chakudya kwa bambo wake ndi kwa abale ake ndi kwa mbumba yonse, potsata kuchuluka kwa ana ao.
13
Njala ija idakula kwambiri, kotero kuti panalibe chakudya pa dziko lonse lapansi, ndipo anthu a ku Ejipito ndi a ku Kanani komwe adafooka nayo njalayo.
14
Yosefe adasonkhanitsa ndalama zonse zimene anthu a ku Ejipito pamodzi ndi a ku Kanani adaamwaza pogula tirigu. Ndalama zonsezo adazitenga napita nazo kunyumba kwa Farao.
15
Ndalama zonse zitaŵathera anthu a ku Ejipito ndi a ku Kanani, Aejipito ambiri adabwera kwa Yosefe, namuuza kuti, “Tipatseniko chakudya! Musatilekerere kuti tife, chitanipo kanthu! Ndalama zathu zonse zatha!”
16
Yosefe adaŵayankha kuti “Bwerani ndi zoŵeta zanu, tidzasinthane ndi chakudya, ngati mukuti ndalama zanu zidatha zonse.”
17
Motero adabwera ndi zoŵeta zao kwa Yosefe, nasinthitsa ndi chakudya zoŵeta zaozo, monga akavalo, nkhosa ndi mbuzi, ng'ombe ndi abulu. Chaka chimenecho Yosefe adaŵapatsa chakudya anthuwo mosinthana ndi zoŵeta zaozo.
18
Chitatha chaka chimenecho, anthuwo adapitanso kwa Yosefe namuuza kuti, “Bwana, ife sitingakubisireni kuti ndalama zathu pamodzi ndi zoŵeta zathu zomwe, zatithera. Palibe chilichonse chotsala choti tingathe kukupatsani, tingodzipereka ifeyo ndi minda yathuyi.
19
Musatilekerere kuti tife m'dziko mwathu, inu mukuwona. Mutipatseko chakudya, ndipo tidzigulitsa ifeyo ndi minda yathu yomwe. Tidzakhala akapolo a Farao, iye adzatenga minda yathu kuti ikhale yake. Mutipatseko mbeu kuti tisafe ndi njala, kutinso minda yathu isakhale masala.”
20
Apo Yosefe adagulira Farao dziko lonse la Ejipito. Mwejipito aliyense adagulitsa minda yake chifukwa njalayo inali itafika poipa kwambiri. Motero dziko lonse lidasanduka la Farao.
21
Yosefe adaŵasandutsa akapolo anthuwo ponseponse m'dziko la Ejipito.
22
Dziko limene sadagule ndi la ansembe lokha. Iwowo sadagulitse dziko lao, popeza kuti Farao ankaŵapatsa chakudya choti azidya.
23
Yosefe adauza anthu kuti, “Onani tsopano ndakugulani pamodzi ndi minda yanu yonse, kugulira Farao. Tsono nazi mbeu, mubzale m'minda mwanu.
24
Pa nthaŵi yokolola mudzapereka kwa Farao chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse pa zokolola zanuzo, ndipo zina zonse zotsala zidzakhala zanu. Zina mudzasungire mbeu, koma zina mudzadye inuyo, mabanja anu ndi antchito anu.”
25
Anthu adayankha kuti, “Mwapulumutsa moyo wathu. Mwatichitira zabwino bwana, tidzakhala akapolo a Farao.”
26
Motero Yosefe adapanga lamulo m'dziko lonse la Ejipito, kuti chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse pa zokolola chidzakhala cha Farao. Lamulo limeneli lilipobe mpaka lero lino. Koma maiko a ansembe okha sadaŵatenge kuti akhale a Farao.
27
Aisraele atakhazikika ku Ejipito, adalemera kwambiri, ndipo adaberekanso ana ambiri.
28
Yakobe adakhala ku Ejipito, zaka 17, choncho zaka za moyo wake zidakwanira 147.
29
Tsono ali pafupi kumwalira, adaitana mwana wake Yosefe namuuza kuti, “Ngati ukundikondadi, undigwire m'kati mwa ntchafu zangazi, ulonjeze kuti udzandikomera mtima ndi kukhulupirika kwa ine, ndipo kuti mtembo wanga sudzauika ku Ejipito kuno.
30
Ndifuna kukagona pamodzi ndi makolo anga. Mtembo wanga udzauchotse ku Ejipito kuno ukauike m'manda a makolo anga.” Yosefe adayankha kuti, “Ndidzachita monga momwe mwaneneramu.”
31
Yakobe adauzanso Yosefe kuti, “Lumbira pamaso panga kuti udzachitadi zimenezi.” Apo Yosefe adalumbiradi, ndipo Yakobe adaŵerama kumutu kwa bedi lake.
← Chapter 46
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 48 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50