bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 15
Genesis 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 16 →
1
Zitatha izi, Chauta adaonekera Abramu m'masomphenya namuuza kuti, “Usachite mantha Abramu, Ine ndili ngati chishango chako chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yaikulu.”
2
Koma Abramu adati, “Ambuye Chauta, ine ndilibe ana. Tsono mungathe bwanji kundipatsa mphotho? Woloŵa m'malo mwanga ndi Eliyezere wa ku Damasikoyu.
3
Simudandipatse ana, motero mmodzi mwa akapolo anga ndiye amene adzalandire chuma changa kuti chikhale choloŵa chake.”
4
Tsono Chauta adamuuza kuti, “Uyu sadzalandira chuma chako kukhala choloŵa chake. Yemwe adzalandire chuma chakochi ndi mwana wako weniweni.”
5
Pomwepo Chauta adatulutsira Abramu panja, namuuza kuti, “Tayang'ana kuthamboku, ndipo uŵerenge nyenyezizo ngati ungathe. Iwe udzakhala ndi zidzukulu zochuluka ngati nyenyezizo.”
6
Apo Abramu adakhulupirira Chauta, ndipo chifukwa cha chimenecho, Chauta adamuwona kuti ndi wolungama.
7
Tsono Chauta adamuuza kuti, “Ine ndine Chauta amene ndidakutulutsa ku Uri wa ku Kaldeya, kuti ndikupatse dziko lino kuti likhale lakolako.”
8
Koma Abramu adati, “Ambuye Chauta, kodi ndingadziŵe bwanji kuti dziko limeneli lidzakhaladi langa?”
9
Chauta adamuyankha kuti, “Tandipatsa ng'ombe ya zaka zitatu, mbuzi ya zaka zitatu, nkhosa ya zaka zitatu, ndiponso njiŵa ndi nkhunda.”
10
Abramu adabwera nazo nyama zonsezo kwa Mulungu, naziduladula pakati. Adaika mabanduwo aŵiriaŵiri mopenyanapenyana, m'mizere iŵiri. Koma mbalame zija sadazidule.
11
Miphamba idadzatera kuti idye nyama zimene adaaphazo, koma Abramu adaipirikitsa.
12
Pamene dzuŵa linkaloŵa, Abramu adagwidwa ndi tulo tofanato, ndiponso adachita mantha kwambiri.
13
Chauta adamuuza kuti, “Udziŵe ndithu kuti zidzukulu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni. Zidzakhala akapolo kumeneko, ndipo zidzazunzika zaka zokwanira 400.
14
Koma mtundu umene udzachite zimenezi, ndidzaulanga, ndipo zidzukulu zakozo potuluka m'dzikomo, zidzatenga chuma chambiri.
15
Tsono iwe udzakhala ndi moyo nthaŵi yaitali ndipo udzafa mwamtendere. Udzaikidwa m'manda utakalamba kwambiri.
16
Patapita mibadwo inai, zidzukulu zakozo zidzabwereranso, chifukwa sindidzaŵathamangitsa Aamori mpaka kuipa kwao kutafika pachimake penipeni kuti adzalangidwe.”
17
Dzuŵa litangoloŵa, kachisisira katagwa, mwadzidzidzi padaoneka mphika wogaduka ndi moto, pamodzi ndi nsakali yoyaka, ndipo ziŵirizi zidadutsa pakati pa nyama zodulidwa zija.
18
Pa tsiku limeneli mpamene Chauta adachita chipangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapatsa zidzukulu zako dziko lonseli kuyambira ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.
19
Ndidzakupatsa dziko la Akeni, la Akenizi, la Akadimoni,
20
la Ahiti, la Aperizi, la Arefaimu,
21
la Aamori, la Akanani, la Agirigasi ndi la Ayebusi.”
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50