bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 37
Genesis 37
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 36
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 38 →
1
Yakobe adakhalabe ku dziko la Kanani kumene bambo wake ankakhala.
2
Mbiri ya banja la Yakobe ndi iyi: Pamene Yosefe anali mnyamata wa zaka 17, ankaŵeta nkhosa ndi mbuzi pamodzi ndi abale ake, ana a Biliha aja ndi a Zilipa, akazi aang'ono a bambo wake. Tsono Yosefeyo ankauza bambo wake zoipa zimene ankachita abale akewo.
3
Israele ankakonda Yosefe kupambana ana ake ena onse, popeza kuti anali mwana wake wapaukalamba. Adamsokera mkanjo wautali wamanja.
4
Abale ake ataona kuti bambo wao ankakonda Yosefe kupambana iwowo, adayamba kudana naye Yosefeyo, ndipo sankalankhula naye mokondwa.
5
Tsiku lina Yosefe adalota maloto, nafotokozera abale ake malotowo. Zitatero, adadana naye kopambana kale.
6
Iye adaŵauza kuti “Mverani maloto omwe ndalota.
7
Tonsefe tinali m'munda, ndipo tinalikumanga mitolo yatirigu. Tilikumanga chomwecho, mtolo wanga unaimirira. Tsono mitolo yanu inauzungulira mtolo wangawo ndi kumauŵeramira.”
8
Apo abale akewo adamufunsa kuti, “Kodi ukuganiza kuti udzakhala mfumu yathu? Kodi ndiye kuti iweyo nkudzatilamula ife?” Motero adadana naye koposa kale chifukwa cha malotowo ndi mau akewo.
9
Tsono Yosefe adalotanso ena maloto, nauzanso abale akewo kuti, “Ndalotanso, ndipo ndaona dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zikundiŵeramira.”
10
Maloto ameneŵa adauzanso bambo wake pamodzi ndi abale ake omwe aja. Atate ake adamdzudzula, adati, “Kodi maloto ameneŵa ngotani? Kodi ukuganiza kuti ine, mai wakoyu pamodzi ndi abale akoŵa, tidzakugwadira iwe?”
11
Tsono abale ake aja adachita naye kaduka kwambiri. Koma atate ake ankakhala akuziganiza zimenezi.
12
Tsiku lina abale ake a Yosefe adapita ku Sekemu kukaŵeta nkhosa za bambo wao.
13
Israele adauza Yosefe kuti, “Abale ako akuŵeta nkhosa ku Sekemu. Ndikufuna kuti upite kwa iwowo.” Yosefe adayankha kuti, “Chabwino, atate.”
14
Tsono bambo wakeyo adamuuza kuti, “Pita ukaŵaone abale ako m'mene aliri, ndiponso ngati zoŵeta zili bwino, kenaka udzandiwuze.” Choncho bambo wake adatuma Yosefe kuchokera ku chigwa cha Hebroni. Yosefe atafika ku Sekemu,
15
munthu wina adampeza akungoyendayenda m'deralo namufunsa kuti, “Kodi ukufunafuna chiyani?” Yosefe adayankha kuti,
16
“Ndikufunafuna abale anga. Chonde tandiwuzani kumene akuŵeta nkhosa.”
17
Munthuyo adati, “Adachoka kale kuno. Ndidaŵamva akunena kuti akupita ku Dotani.” Apo Yosefe adaŵalondola abale akewo, nakaŵapeza ku Dotani.
18
Abale ake aja adamuwonera kutali, iye asanayandikire nkomwe pamene panali iwopo. Adayamba kumpangira chiwembu natsimikiza zoti amuphe.
19
Onsewo ankauzana kuti, “Uyotu kamaloto uja, akudza apoyo!
20
Tiyeni timuphe, mtembo wake tiwuponye m'chitsime china mwa zitsime zili apazi. Tizikanena kuti wajiwa ndi chilombo, ndipo tidzaone tanthauzo lake la maloto ake aja.”
21
Tsono Rubeni adamva zimene enawo ankanena, ndipo adayesetsa kumpulumutsa Yosefe. Adati, “Ai tisamuphe, tisakhetse magazi ake.
22
Tingomuponya m'chitsime chopanda madzichi kuchipululu konkuno. Tisampweteke konse.” Ankanena zimenezi akuganiza zomupulumutsa m'manja mwao, kuti amtumize kwa bambo wake.
23
Yosefe atafika kumene kunali abale akewo, iwowo adamuvula mkanjo wake, uja wautali wamanjawu umene adaavala,
24
namtenga, nkumuponya m'chitsime chopanda madzi.
25
Pamene iwo ankadya, adaona gulu la Aismaele akuchokera ku Giliyadi. Ngamira zao zinali zitasenza nzonono ndi zonunkhira zimene ankapita nazo ku Ejipito.
26
Tsono Yuda adafunsa abale ake kuti, “Kodi tipindulanji tikamupha mbale wathuyu ndi kubisa, osaulula kuti tamupha?
27
Tiyeni timgulitse kwa Aismaeleŵa. Nanga iyeyu si mbale wathu, thupi limodzi ndiponso magazi amodzi?” Abale akewo adavomereza zimenezo.
28
Tsono Amidiyani ena amalonda adafika pomwepo. Abale akewo adamtulutsa Yosefeyo m'chitsime muja, namgulitsa kwa Aismaelewo pamtengo wokwana masekeli a siliva makumi aŵiri, ndipo iwowo adapita naye ku Ejipito.
29
Rubeni atabwerera kuchitsime kuja, adapeza muli ng'waa! Pomwepo adang'amba zovala zake chifukwa cha chisoni.
30
Ndipo adabwerera kwa abale ake aja naŵauza kuti, “Mnyamata ujatu palibe! Tsono ine ndichite chiyani?”
31
Pomwepo iwo adapha mbuzi, naviika mkanjo wa Yosefe uja m'magazi ake.
32
Adatenga mkanjowo napita nawo kwa bambo wao, nati, “Tayang'anani, kapena nkukhala mkanjo wa mwana wanu uja.”
33
Yakobe adauzindikira mkanjowo, nati, “Ha, ndi wakedi! Chilombo chamupha mwana wanga. Kalanga ine, Yosefe wakadzulidwa!”
34
Yakobe adang'amba zovala zake, navala chiguduli m'chiwuno, chifukwa cha chisoni. Adalira maliro a mwana wakeyo nthaŵi yaitali.
35
Ana ake onse aamuna ndi aakazi, adabwera kuti amtonthoze koma iye adakana, adati, “Ndidzakhala ndikulira mwana wanga mpaka kumanda komwe kuli iyeko.” Choncho adapitirirabe kulira chifukwa cha Yosefe mwana wake.
36
Nthaŵi imeneyo nkuti Amidiyani aja atamgulitsa Yosefe kwa Potifara ku Ejipito. Potifarayo anali mmodzi mwa nduna za Farao, ndipo anali mkulu wa asilikali olonda kunyumba kwa Farao.
← Chapter 36
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 38 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50