bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 50
Genesis 50
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 49
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
1
Pomwepo Yosefe adadzigwetsa pa mtembo wa bambo wake akulira, kwinaku akumpsompsona bambo wake.
2
Tsono Yosefeyo adalamula asing'anga kuti akonze ndi mankhwala mtembo wa bambo wake, kuti usaole, ndipo iwowo adachitadi zimenezo.
3
Ntchitoyo idaŵatengera masiku 40, monga kunkafunikira pa ntchito ya mtundu umenewo. Aejipito adalira maliro a Israele masiku 70.
4
Yosefe atatha kulira maliro a bambo wake, adauza nduna za Farao kuti, “Chonde mundikomere mtima, Farao mukamuuze kuti,
5
‘Pamene bambo wanga anali pafupi kufa, adandilumbiritsa kuti ndikamuike m'manda amene adadzikumbira m'dziko la Kanani. Motero chonde, mundilole kuti ndipite ndikaike bambo wanga, pambuyo pake ndidzabweranso.’ ”
6
Farao adamuyankha kuti, “Pita ukaike atate ako monga momwe adakulumbiritsira.”
7
Yosefe adapita kukaika bambo wake. Ndipo nduna zonse za Farao, akuluakulu a bwalo, ndi anthu ena otchuka a ku Ejipito adamperekeza.
8
Adapitanso ndi onse a banja lake, abale ake, ndi onse a banja la bambo wake. Ku Goseni kuja kudangotsala ana okhaokha, nkhosa zao, abusa ndi ng'ombe zao.
9
Asilikali okwera pa magaleta ndi akavalo, nawonso adamperekeza. Motero chinali chinamtindi cha anthu.
10
Atafika ku malo opunthira tirigu ku Atadi, kuvuma kwa Yordani, adachita mwambo waulemu wamaliro, ndipo adalira maliro kumeneko masiku asanu ndi aŵiri.
11
Tsono nzika za ku Kanani zitaona kulira koteroko ku Atadi kuja, zidati, “Kulira kwa maliro kotereku ndi kwa ku Ejipito.” Nchifukwa chake malowo adaŵatchula kuti Abele-Miziraimu, ali kuvuma kwa Yordani.
12
Ana a Yakobe adachitadi monga momwe bambo wao adaaŵalamulira.
13
Adamnyamula kupita ku Kanani, nakamuika m'phanga limene linali m'munda ku Makipera, kuvuma kwa Mamure. Abrahamu adagula phangalo kwa Efuroni Muhiti pamodzi ndi munda womwewo, kuti pakhale manda.
14
Yosefe ataika bambo wake m'manda, adabwerera ku Ejipito ndi abale ake aja, pamodzi ndi onse amene adamperekeza.
15
Atamwalira bambo wao uja, abale ake a Yosefe adati, “Nanga tidzatani ife, Yosefe akadzayamba kudana nafe ndi kufuna kubwezera zoipa zonse zimene tidamuchita zija?”
16
Motero adatumiza mau kwa Yosefe kuti, “Atate anu asanafe adanena mau akuti,
17
‘Ndikumpempha Yosefe kuti akhululukire cholakwa cha abale ake chimene adamchitira.’ Pepani tsopano tikhululukireni cholakwa chimene ife, akapolo a Mulungu wa atate anu, tidachita.” Atangomva zimenezi Yosefe adayambapo kulira.
18
Tsono abale ake adabwera nagwada pamaso pake. Adati, “Ife tili pamaso panu ngati akapolo anu.”
19
Koma Yosefe adaŵauza kuti, “Musaope ai. Ine sindingathe kudziika m'malo mwa Mulungu.
20
Inu mudaapangana kuti mundichite chiwembu, koma Mulungu adazisandutsa kuti zikhale zabwino ndipo kuti zipulumutse moyo wa anthu ambiri. Choncho onsewo ali moyo lero lino chifukwa cha zimenezo.
21
Tsopano inu musade nkhaŵa. Ndidzakusamalani pamodzi ndi ana anu omwe.” Motero adaŵalimbitsa mtima naŵasangulutsa.
22
Yosefe adakhala ku Ejipito pamodzi ndi mbumba ya atate ake. Pamene ankamwalira nkuti ali wa zaka 110.
23
Adakhala moyo mpaka kuwona adzukulu ake, ana a Efuremu. Pamene ana a Makiri mwana wa Manase adabadwa, Yosefe adaŵalandira m'banja mwake.
24
Ndipo adauza abale ake aja kuti, “Patsala pang'ono kuti ndikusiyeni, koma Mulungu adzakusungani ndithu, ndipo adzakutulutsani m'dziko muno, kupita nanu ku dziko limene adaalonjeza Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.”
25
Kenaka Yosefe adapempha ana a Israele kuti alumbire. Adati, “Lonjezeni kuti Mulungu akakusungani, mudzasenza mafupa anga kuchoka nawo kuno.”
26
Motero Yosefe adamwalira ali wa zaka 110. Mtembo wake adaukonza ndi mankhwala, naukhazika m'bokosi ku Ejipito komweko.
← Chapter 49
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50