bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 12
Genesis 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 13 →
1
Tsiku lina Chauta adauza Abramu kuti, “Choka kudziko kwako kuno. Usiye abale ako ndi banja la bambo wako, ndipo upite ku dziko limene nditi ndikusonyeze.
2
Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena.
3
“ Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe, koma ndidzatemberera aliyense wokutemberera. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.”
4
Abramu anali wa zaka 75 pamene ankachoka ku Harani monga Chauta adaamlamulira, ndipo Loti adapita naye limodzi.
5
Abramu adatenga mkazi wake Sarai, Loti mwana wa mng'ono wake, pamodzi ndi chuma chake chonse, ndi antchito amene adaali nawo ku Harani. Adayamba ulendo wonka ku Kanani. Atafika ku Kanani,
6
Abramuyo adayendera dziko lonselo mpaka adakafika ku Sekemu, ku mtengo wa thundu wa ku More. Pa nthaŵi imeneyo nkuti Akanani akadalimo m'dzikomo.
7
Chauta adaonekera Abramu namuuza kuti, “Dziko limeneli ndidzapatsa zidzukulu zako.” Choncho pa malo amenewo Abramu adamanga guwa, kumangira Chauta amene adaamuwonekera.
8
Pambuyo pake adasendera ku mapiri a kuvuma kwa Betele, ndipo adamanga hema lake pakati pa Betele chakuzambwe ndi Ai chakuvuma. Kumenekonso adamangako guwa, ndipo adatama dzina la Chauta mopemba.
9
Adapitirira ulendo wake pang'onopang'ono, kuloŵera ku Negebu, chigawo chakumwera.
10
Koma m'dziko limenelo mudagwa njala. Ndipo chifukwa choti njala idaakula kwambiri, Abramu adapitirira ndithu chakumwera, mpaka kukafika ku Ejipito, nakhala kumeneko kanthaŵi.
11
Pamene anali pafupi kuwoloka malire a Ejipito, adauza mkazi wake Sarai kuti, “Ndikudziŵa kuti iwetu ndiwe mkazi wokongola.
12
Ndipo Aejipito akakupenya, aziti, ‘Ameneyu ndi mkazi wake,’ tsono kuti akukwatire iwe, andipha ineyo.
13
Chonde, uzikaŵauza kuti, ‘Ndi mlongo wanga.’ Motero zonse zidzandiyendera bwino chifukwa cha iwe, ndipo ndidzapulumuka.”
14
Abramu ataoloka malire kuloŵa mu Ejipito, Aejipito adaonadi kuti mkazi wake ndi wokongola kwambiri.
15
Akalonga a mfumu ya ku Ejipito atamuwona mkaziyo, adakauza Farao za kukongola kwake. Pomwepo anthu aja adamtenga mkaziyo kukamuika ku nyumba ya mfumu.
16
Ndipo Farao adamchitira zabwino Abramu uja chifukwa cha mkaziyo, nampatsa nkhosa, mbuzi, ng'ombe, abulu, ngamira ndiponso akapolo aamuna ndi aakazi.
17
Koma Chauta adagwetsa nthenda zoopsa pa Farao ndi pa anthu a m'nyumba mwake omwe, chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu.
18
Apo Farao adaitana Abramu namufunsa kuti, “Kodi iwe, wandichita zotani? Bwanji osandiwuza kuti ameneyu ndi mkazi wako?
19
Bwanji umanena kuti ndi mlongo wako kuti ine ndimukwatire? Nayu mkazi wako. Mtenge, ndipo uchoke!”
20
Farao adalamula anthu ake, ndipo iwowo adatulutsa Abramu ndi mkazi wake m'dzikomo, pamodzi ndi zonse zimene anali nazo.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50