bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 38
Genesis 38
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 39 →
1
Nthaŵi imeneyo Yuda adachoka nakakhala kwa munthu wina wa fuko la Adulamu dzina lake Hira.
2
Kumeneko Yuda adaonako mtsikana Wachikanani, mwana wa Suwa, namkwatira.
3
Mkaziyo adatenga pathupi nabala mwana wamwamuna, nkumutcha Ere.
4
Adatenganso pena pathupi nabala mwana wamwamuna, nkumutcha Onani.
5
Adabalanso mwana wina wamwamuna, namutcha Sela. Pamene Sela ankabadwa, nkuti Yuda ali ku Kezibu.
6
Yuda adampezera mkazi mwana wake wachisamba uja Ere, dzina lake Tamara.
7
Koma makhalidwe oipa a Ere adaipira Chauta, mwakuti Chauta adamlanga ndi imfa.
8
Motero Yuda adauza Onani kuti, “Loŵana naye mkazi wamasiye wa mbale wakoyu. Uloŵe chokolo ndithu, kuti mbale wakoyo akhale ndi ana.”
9
Koma Onani adaadziŵa kuti anawo sadzakhala ake. Motero nthaŵi zonse akamakhala naye mkaziyo, ankangotayira pansi mbeu yake, kuti asamubalire ana mbale wakeyo.
10
Tsono zimene ankachitazo zidaipira Chauta ndipo Chauta adamlanganso ndi imfa.
11
Apo Yuda adauza mpongozi wake uja Tamara kuti, “Bwererani kunyumba kwa bambo wanu, mukakhale wamasiye kumeneko mpaka mwana wanga Sela atakula.” Adanena zimenezi chifukwa ankaopa kuti Sela angafenso monga abale akewo. Motero Tamara adabwerera kunyumba kwa bambo wake.
12
Patapita nthaŵi, mkazi wa Yuda uja, mwana wa Suwa, adamwalira. Tsono Yuda atatha kulira malirowo, iyeyo pamodzi ndi bwenzi lake Hira Mwadulamu, adapita ku Timna kumene ankameta nkhosa zake.
13
Munthu wina adauza Tamara kuti, “Apongozi ako akupita ku Timna kukameta nkhosa.”
14
Tsono Tamarayo adasintha zovala zake zaumasiye zija navala zina. Adadziphimba kumaso ndi nsalu, nakakhala pansi pa chipata cha ku Enaimu. Mudzi wa Enaimu unali pa mseu wopita ku Timna. Adaadziŵa kuti pa nthaŵiyo nkuti Sela atakula, komabe Tamara anali asanamloŵe chokolo Sela uja.
15
Yuda atamuwona, adaamuyesa mkazi wadama, chifukwa anali atadziphimba kumaso.
16
Adapita ku mbali ya mseu komwe kunali iyeyo namuuza kuti, “Kodi mungandilole kuti ndigone nanu?” Yuda sankadziŵa kuti ndi mpongozi wake. Mkaziyo adati, “Mudzandipatsa chiyani?”
17
Yuda adayankha kuti, “Ndidzakutumizira mbuzi yaing'ono ya m'khola mwanga.” Tsono Tamarayo adati, “Chabwino, ndivomera mukandipatsa chikole choti mpaka mudzanditumizire.”
18
Yuda adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna chikole chotani?” Tamara adayankha kuti, “Mundipatse mphete yanu pamodzi ndi chingwe chanu chomwecho, ndi ndodo yanu yoyendera imene ili m'manja mwanuyi.” Yuda adapereka zonsezo kwa Tamara. Atatero Yuda adagona naye mkaziyo, ndipo adatenga pathupi.
19
Tsono Tamara adanyamuka nachokapo. Adachotsa nsalu imene adaadziphimba nayo kumaso ija, navalanso zovala zake zaumasiye zija.
20
Pambuyo pake Yuda adatuma bwenzi lake kukapereka mbuzi ija, kuti mkazi uja amubwezere zikole zija. Koma bwenzi lakeyo sadakampeze mkaziyo.
21
Adafunsa anthu akomweko kuti, “Kodi mkazi wadama amene ankakhala pambali pa mseu wopita ku Enaimu uja ali kuti?” Anthuwo adayankha kuti, “Chikhalire sipadakhale mkazi wadama pa malo amenewo.”
22
Adabwerera kwa Yuda nakamuuza kuti, “Sindidampeze mkazi uja, ndipo anthu akumeneko andiwuza kuti, ‘Chikhalire sipadakhale mkazi wadama pa malo amenewo.’ ”
23
Yuda adati, “Zinthu zimenezo atenge zikhale zake, kuwopa kuti anthu angadzatiseke. Ngakhale sudampeze mkaziyo, komabe ine ndidaamtumizira ndithu mbuziyi.”
24
Patapita miyezi itatu, munthu wina adauza Yuda kuti, “Mpongozi wanu uja Tamara adachita chigololo, ndipo ali ndi pathupi.” Pomwepo Yuda adalamula kuti, “Kamtengeni ndipo mukamtenthe kuti afe.”
25
Akutengedwa kumene, Tamarayo adatumiza mau kwa Yuda mpongozi wake kuti, “Ine ndili ndi pathupi pa mwiniwake zinthu izi. Taziyang'anani, muwone mwina inu nkumudziŵa mwiniwakeyo kuti ndani: mpheteyi ndi chingwechi ndiponso ndodo yoyenderayi.”
26
Yuda atazizindikira zinthuzo adati, “Akunenetsadi. Ndine amene ndidalakwa. Bwenzi nditampereka kwa mwana wanga Sela kuti amkwatire.” Choncho Yuda sadagone nayenso mkaziyo.
27
Itakwana nthaŵi yakuti Tamara achire, m'mimba mwake munali mapasa.
28
Pa nthaŵi yochira, mmodzi mwa anawo adatulutsa dzanja. Mzamba adaligwira, nalimanga ndi chingwe chofiira nati, “Ameneyu ndiye woyamba kubadwa.”
29
Koma mwanayo adalibweza dzanja lake, mwakuti mbale wake ndiye adayambira kubadwa. Tsono mzamba uja adati, “Uchita kudziphothyolera wekha chotere!” Motero mwanayo adatchedwa Perezi.
30
Pambuyo pake mbale wake adabadwa chingwe chofiira chija chili lende ku dzanja. Tsono iyeyu adatchedwa Zera.
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 39 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50