bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 18
Genesis 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 19 →
1
Chauta adaonekera Abrahamu ku mitengo ya thundu ya ku Mamure ija. Abrahamuyo atakhala pa khomo la hema lake nthaŵi yamasana kutatentha,
2
mwadzidzidzi adangoona anthu atatu ataimirira potero. Atangoŵaona, adanyamuka mwamsanga kukaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu,
3
nati, “Mbuyanga, ngati ndapeza kuyanja pamaso panu, chonde musapitirire pakhomo pa mtumiki wanu.
4
Ndikupatseni madzi kuti mutsuke mapazi. Mungathe kubapuma patsinde pa mtengo pano.
5
Ine tsopano ndikatenga chakudya, kuti mukadya mupeze mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Mwabwera pakhomo panga pano, motero ndiyenera kukutumikirani.” Anthuwo adayankha kuti, “Chabwino, uchite monga waneneramo.”
6
Abrahamu adaloŵa msangamsanga m'hema, nauza Sara kuti “Utenge msanga nsengwa zitatu za ufa wosalala, uukande ndi kupanga buledi.”
7
Pamenepo Abrahamu adathamanga nakatenga mwanawang'ombe wonenepa, nampereka kwa wantchito kuti akonze mwamsanga.
8
Kenaka adatenga chambiko ndi mkaka wokama chatsopano, ndi nyama yokonzakonza ija naŵapatsa zonsezo. Iye adakhala potero pamene anthuwo analikudya patsinde pa mtengo.
9
Tsono anthuwo adafunsa Abrahamu kuti, “Kodi mkazi wako Sara ali kuti?” Abrahamu adayankha kuti, “Ali m'hemamu.”
10
Chauta adati, “Ndikukulonjeza kuti pakapita miyezi isanu ndi inai ndidzabweranso, ndipo mkazi wako adzakhala ali ndi mwana wamwamuna.” Sara ankangomvetsera ali kuseri kwa chitseko cha hema.
11
Abrahamu pamodzi ndi Sara anali nkhalamba zokhazokha, ndipo nthaŵi imeneyo nkuti Sara ataleka kusamba monga amachitira akazi.
12
Motero Sara adangoseka, namati, “Ha, monga ndakalambira inemu, kodi nkuthekanso kuti ndikondwe ndi mwamuna wanga? Komanso mwamuna wanga ndi wokalamba zedi.”
13
Chauta adafunsa Abrahamu kuti, “Chifukwa chiyani Sara amaseka ndi kunena kuti, ‘Ine monga ndakalambiramu kungatheke bwanji kukhala ndi mwana?’
14
Kodi chilipo china choti chingakanike Chauta? Tsono pa nthaŵi yake, ndidzachitadi zimene ndalonjezazi, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
15
Apo Sara adakana chifukwa cha mantha, adati, “Sindidaseke.” Koma Iye adati, “Inde, unaseka.”
16
Tsono anthuwo adachoka, nafika pamalo pamene anali kupenya Sodomu. Abrahamu adapita nawo limodzi, naŵalozera njira.
17
Ndipo Chauta adanena mwa Iye yekha kuti, “Abrahamuyu sindingamubisire chomwe ndikuti ndichite.
18
Zidzukulu zake zidzakhala mtundu waukulu wamphamvu. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadalitsidwa chifukwa cha iye.
19
Ndamsankha iyeyu kuti alamule ana ake ndi mabanja ake akutsogolo kuti azidzamvera mau anga, pochita zabwino ndi zolungama. Choncho ndidzachita zonse zimene ndidamlonjeza.”
20
Tsono Chauta adauza Abrahamu kuti, “Pali zolakwa zoopsa zokhudza Sodomu ndi Gomora, ndipo tchimo lao ndi lalikulu kwambiri.
21
Choncho ndikuti nditsikireko kuti ndikaone ngati zolakwa zimene ndamvazo ndi zoona. Ngati si choncho, ndidzadziŵa.”
22
Anthu aja adachoka, napita ku Sodomu, koma Abrahamu adatsarira ndi Chauta.
23
Apo Abrahamu adayandikira kwa Chauta namufunsa kuti, “Kodi monga mudzaonongadi anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa?
24
Nanga patakhala kuti pali anthu 50 osachimwa mumzindamo, kodi mudzaonongabe mzinda wonse? Kodi simudzauleka kuti musunge anthu 50 amenewo?
25
Ndithu simudzaononga anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa. Chimenechi nchosatheka ndipo simungachite. Mukadatero bwenzi anthu osachimwa akulangidwira kumodzi ndi ochima. Kutalitali, Inu simungachite zotere! Kodi Muweruzi wa dziko lonse lapansi nkupanda chilungamo?”
26
Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 50 osachimwa m'Sodomu, ndidzauleka mzinda wonsewo osauwononga, chifukwa cha anthu 50 amenewo.”
27
Abrahamu adalankhulanso, adati, “Chonde, ndalimba mtima pakulankhula nanu chotere, Ambuye. Inetu ndine munthu chabe pamaso panu.
28
Nanga pa chiŵerengero cha 50 pakangopereŵera anthu asanu okha, bwanji? Kodi mudzaononga mzindawo popeza kuti asoŵa asanu okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 45 olungama, sindidzaononga mzindawo.”
29
Abrahamu adafunsanso kuti, “Nanga pakapezeka anthu olungama 40 okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 40, sindidzauwononga.”
30
Apo Abrahamu adati, “Chonde ndapota nanu, musapse mtima, Ambuye, tsopano ndifunsanso. Nanga mutapezeka anthu olungama 30?” Chauta adati, “Ndikapeza anthu 30, sindidzauwononga.”
31
Tsono Abrahamu adati, “Ndapota nanu, khululukireni kulimba mtima chotere polankhula ndi Inu Ambuye. Nanga mutapezeka olungama 20?” Chauta adati, “Ndikapeza anthu olungama 20, sindidzauwononga mzindawo.”
32
Abrahamu adati, “Chonde, musandikwiyire Ambuye, koma ndilankhule kamodzi kokhaka. Nanga mutapezeka khumi okha?” Aponso Chauta adati, “Ndikapeza olungama khumi, sindidzauwononga mzindawo.”
33
Chauta atatha kulankhula ndi Abrahamu, adachokapo, Abrahamuyo nkumabwerera kwao.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50