bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 31
Genesis 31
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 32 →
1
Yakobe adamva kuti ana a Labani ankanena kuti, “Yakobe watenga zonse za bambo wathu. Wapeza chuma chake m'chuma cha bambo wathu.”
2
Yakobe adazindikiranso kuti Labani sankamuwonetsa nkhope yabwino ngati kale.
3
Tsono Chauta adamuuza kuti, “Bwerera ku dziko la atate ako ndi kwa abale ako. Ine ndidzakhala nawe.”
4
Tsono Yakobe adatumiza mau kwa Rakele ndi kwa Leya kuti akakumane naye kubusa kumene kunali zoŵeta zake.
5
Atafikako, iye adaŵauza kuti, “Ndaona kuti bambo wanu tsopano sakundipenya ndi maso abwino ngati kale. Koma Mulungu wa atate anga wakhala nane.
6
Nonse aŵirinu mukudziŵa bwino kuti ndidagwira ntchito kwa bambo wanu ndi mphamvu zanga zonse.
7
Komabe iye wandipusitsa, ndipo malipiro anga waasinthasintha kakhumi konse. Koma Mulungu sadamlole kuti andichite choipa.
8
Nthaŵi zonse Labani akanena kuti, ‘Zoŵeta zamathothomathotho zidzakhala malipiro ako,’ zoŵeta zonse zinkakhala zamathothomathotho. Ndipo akanena kuti, ‘Zamipyololo zikhala malipiro ako,’ zoŵeta zonse zinkangokhala zamipyololo.
9
Mulungu watenga zoŵeta zonse kwa bambo wanu, wapatsa ine.
10
Pa nthaŵi yakuti zoŵeta zitenga maŵere, ine ndidalota maloto, ndipo ndidaona kuti atonde amene ankakwerawo anali amipyololomipyololo, amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga.
11
Ndipo mngelo wa Mulungu adalankhula nane m'maloto momwemo nandiitana kuti, ‘Yakobe,’ ine ndidayankha kuti, ‘Ee Ambuye!’
12
Iye adati, ‘Tayang'ana, ndipo upenye kuti atonde onse amene akukweraŵa ndi amipyololomipyololo, amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga. Zimenezi ndachita ndine, popeza kuti ndaona zimene Labani akukuchita.
13
Ine ndine Mulungu amene ndidakuwonekera ku Betele kuja kumene udaimika mwala wachikumbutso ndi kuudzoza mafuta, ndipo kumeneko iwe udalumbira. Konzeka tsopano, uchoke kuno, ubwerere ku dziko lakwanu.’ ”
14
Rakele ndi Leya adayankha kuti, “Palibe chomwe chatitsalira ife kwa bambo wathu choti chikhale choloŵa chathu.
15
Ife bambo wathu akutiyesa alendo. Adatigulitsa, ndipo ndalama zomwe adazipezera pa ifezo, adamwaza zonse.
16
Chuma chonse chimene Mulungu wachotsa kwa bambo wathu, ndi chathu ndi cha ana athu. Chitani zimene Mulungu wakuuzani.”
17
Motero Yakobe adakonzekera kuti achoke, kubwerera kwa bambo wake ku dziko la Kanani. Tsono ana ake onse pamodzi ndi akazi ake omwe adaŵakweza pa ngamira.
18
Ndipo zoŵeta zonse adazitsogoza namazikusa, pamodzi ndi zonse zimene adazipeza ku Mesopotamiya kuja.
19
Labani anali atapita kokameta nkhosa. Ndipo akadali komweko, Rakele adaba timilungu ta m'nyumba mwa Labani, bambo wake.
20
Motero Yakobe adampusitsa Labani Mwaramu uja posamuuza kuti akuchoka.
21
Adatenga zake zonse, nachoka chothaŵa. Adanyamuka, naoloka mtsinje wa Yufurate, nkuyamba ulendo wopita ku dziko lamapiri la Giliyadi.
22
Patapita masiku atatu, Labani adamva kuti Yakobe adathaŵa.
23
Tsono adatenga anthu ake, nkulondola Yakobeyo masiku asanu ndi aŵiri, mpaka adakampezera ku dziko lamapiri la Giliyadi.
24
Labani Mwaramu uja adalota maloto usiku womwewo. Mulungu adadza namuuza kuti, “Usamuwopseze Yakobe mwa njira iliyonse.”
25
Labani adampeza Yakobe atamanga mahema kumapiriko. Nayenso Labaniyo adamanga mahema ake komweko ku dziko lamapiri la Giliyadi.
26
Labani adafunsa Yakobe kuti, “Chifukwa chiyani wandinyenga ndi kutenga ana anga aakazi ngati ogwidwa pa nkhondo?
27
Chifukwa chiyani wandinyenga ndi kundizemba osandiwuza? Ukadandiwuza, bwenzi nditakulola mokondwa, ndipo bwenzi pali kumaimba nyimbo ndi ting'oma ndi azeze.
28
Sudandilole kuti nditsazikane ndi adzukulu anga ndi ana anga. Udachita zopusa.
29
Ndili nazo mphamvu zakukuchita choipa. Koma usiku wapitawu, Mulungu wa atate ako wandiwuza kuti, ‘Usamuwopseze Yakobe mwa njira iliyonse.’
30
Ndikudziŵa kuti udachoka chifukwa unkafunitsitsa kubwerera kwanu. Koma bwanji wandibera timilungu tanga?”
31
Yakobe adayankha kuti, “Ndinkaopa, chifukwa ndinkaganiza kuti mundilanda ana anuŵa.
32
Koma mukapeza kuti wina aliyense pano ali ndi timilungu tanu, aphedwe ameneyo. Anthu tili nawoŵa akhale mboni pano pamene inu muyang'ane zinthu zanu m'katundu yenseyu. Tsono mukazipeza zanuzo mutenge.” Monsemo nkuti Yakobe ali wosadziŵa kuti Rakele adaaba timilunguto.
33
Labani adakaloŵa m'hema la Yakobe ndi m'hema la Leya ndiponso m'hema la adzakazi aŵiri aja, koma sadatipeze timilungu taketo. Kenaka adakaloŵa m'hema la Rakele.
34
Rakeleyo anali ataibisa milungu ya m'nyumba mwa Labaniyo, ataiika pa chishalo cha pamsana pa ngamira, iyeyo nkukhala pomwepo. Labani adafunafuna m'hema monsemo, koma osaipeza.
35
Rakele adauza bambo wake kuti, “Ngati ndikulephera kuimirira pamaso panu, musandikwiyire bambo, chifukwa sindili bwino malinga nza ife akazife.” Motero Labani adalephera kutipeza timilungu ta m'nyumba mwake tija.
36
Apo Yakobe adapsa mtima kwambiri ndipo adalankhula ndi Labani mokalipa, adati, “Kodi ndakulakwirani chiyani? Kodi ndaphwanya lamulo lotani, kuti mundilondole?
37
Tsono mwafunafuna m'katundu wanga yense, kodi mwapeza chiyani chanu? Chomwe mwapezacho muchiike poyera pano, kuti anthu anu ndi anthu angaŵa achiwone. Ndipo iwowo ndiwo aone wokhoza pakati pa aŵirife.
38
Ndakhala nanu zaka makumi aŵiri tsopano, ndipo nkhosa zanu pamodzi ndi mbuzi zomwe sizidapolozepo ai. Ine sindidadyeko nkhosa za m'khola mwanu.
39
Nkhosa ikajiwa ndi zilombo, ine ndinkalipira nthaŵi zonse, sindinkabwera nayo kwa inu, kuwonetsa kuti sindidalakwe. Munkafuna kuti ndilipire chilichonse chobedwa usiku kapena usana.
40
Nthaŵi zambiri ndinkavutika ndi kutentha masana ndiponso ndi kuzizira usiku. Sindinkatha kuwona tulo.
41
Umu ndi m'mene zidaaliri zinthu pa zaka makumi aŵiri zomwe ndidakhala ndi inu. Ndidakugwirirani ntchito zaka khumi ndi zinai chifukwa cha ana anu aŵiriŵa, ndipo zaka zisanu ndi chimodzi ndidagwirira zoŵeta. Komabe malipiro anga mwakhala mukusintha kakhumi konse.
42
Mulungu wa atate anga, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu amene Isaki ankamuwopa, akadapanda kukhala nane, bwenzi mutandichotsa kale ndili chimanjamanja. Koma Mulungu adaona mavuto anga ndi ntchito za manja anga, ndipo usiku wapitawu Iye wakutsutsani.”
43
Labani adayankha Yakobe kuti, “Ana aakaziŵa ndi anga, ana ao ndi anga, pamodzi ndi zoŵeta zomwezi. Zonse ukuziwonazi nzanga. Koma tsopano ndiŵachitire chiyani ana anga aakaziŵa pamodzi ndi ana aoŵa?
44
Chabwino, tiye tichite chipangano, chikhale mboni pakati pa ine ndi iwe.”
45
Yakobe adaimiritsa mwala.
46
Adauza anthu ake kuti asonkhanitse miyala, aunjike mulu. Ndipo pambali pake pa muluwo adadyerapo chakudya.
47
Tsono muluwo Labani adautcha Yagara-Sahaduta, koma mulu womwewo Yakobe adautcha Galedi.
48
Pambuyo pake Labani adati, “Mulu wamiyalawu udzakhala chikumbutso kwa ine ndi iwe.” Nchifukwa chake malowo adaŵatcha Galedi.
49
Labani adanenanso kuti, “Chauta atiyang'anire ife tonse aŵiri pamene tikulekana. Motero malowo adaŵatcha Mizipa.
50
Labani adapitirira kunena kuti, Ukamakaŵazunza ana angaŵa, kapena ukakakwatira akazi ena, ngakhale palibe wina ali nafe pano, ukumbukire kuti Mulungu ndiye mboni pakati pa ine ndi iwe.”
51
Tsono Labani adauza Yakobe kuti, “Pano pali miyala imene ndaunjika pakati pathu, ndipo pompano pali mwala wachikumbutso.
52
Mulu umenewu pamodzi ndi mwala wachikumbutsowu, zonsezi ndi mboni. Ine sindidzapyola mulu umenewu kuti ndilimbane nawe. Iwenso usadzapyole muluwu kuti ulimbane ndi ine.
53
Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate ao, ndiye adzatiweruze ife aŵiri.” Motero Yakobe adalumbira m'dzina la Mulungu amene Isaki bambo wake ankamuwopa.
54
Tsono Yakobe adapereka nsembe paphiripo, naitana anthu ake kuti adzadye chakudya. Atamaliza kudyako, adagona paphiri pomwepo.
55
M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Labani adampsompsona adzukulu ake aja pamodzi ndi ana ake aakaziwo naŵatsazika, ndipo ataŵadalitsa adachoka namapita kwao.
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 32 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50