bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 21
Genesis 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 22 →
1
Chauta adakumbukira Sara namchitira zimene adaamulonjeza.
2
Choncho Sarayo adatenga pathupi, nabalira Abrahamu mwana wamwamuna pamene Abrahamuyo anali nkhalamba. Mwana ameneyu adabadwa pa nthaŵi yeniyeni imene Mulungu adaanena.
3
Ndipo mwana wa Abrahamuyo, mwana amene Sara adamubalirayo, Abrahamu adamutcha Isaki.
4
Abrahamu adamuumbala mwanayo ali wa masiku asanu ndi atatu, monga momwe Mulungu adaalamulira.
5
Abrahamu nkuti ali wa zaka 100 pamene Isakiyo adabadwa.
6
Tsono Sara adati, “Mulungu wandikondweretsa ndi kundiseketsa. Aliyense amene adzamve zimenezi, adzakondwera nane.”
7
Ndipo adati, “Akadadziŵa ndani kuti Sara nkuyamwitsa mwana? Komabe ndamubalira mwana wamwamuna Abrahamu pamene ali nkhalamba.”
8
Mwanayo adakula, ndipo pa tsiku lakuti amuletsa kuyamwa, Abrahamu adachita phwando lalikulu.
9
Tsiku lina Ismaele, amene Hagara Mwejipito uja adabalira Abrahamu, ankamunyoza Isaki mwana wa Sara.
10
Sara ataona, adauza Abrahamu kuti, “Mchotseni mdzakaziyu pamodzi ndi mwana wake yemweyu. Mwana wa mdzakazi asadzalandireko chuma chanu chimene adzalandire mwana wanga Isaki.”
11
Zimenezi zidamuvuta kwambiri Abrahamu, chifukwa chakuti Ismaele nayenso anali mwana wake.
12
Koma Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Mtima wako usavutike chifukwa cha mwanayo ndi mzikazi wako Hagara. Zonse zimene akukuuza Sara uchite, chifukwa Isakiyu ndi amene adzakhala kholo la zidzukulu zako monga momwe ndidakulonjezera.
13
Mwana wa mdzakaziyunso ndidzampatsa ana ambiri, ndipo adzasanduka mtundu ndithu, popeza kuti iyeyunso ndi mwana wako.”
14
M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abrahamu adapatsa Hagara chakudya ndi thumba lachikopa la madzi. Kenaka adatenga mwanayo nabereketsa Hagara, ndipo atatero adamuuza kuti azipita. Hagara adachokadi, nkumangoyendayenda m'chipululu cha Beereseba.
15
Tsono madzi aja atamthera, adangosiya mwanayo pa chitsamba.
16
Iye adakakhala pansi poteropo, pa mtunda wa mamita 100, chifukwa ankati, “Ine sindingathe kumaonerera mwana wanga alikufa chotere.” Ali pansi pomwepo, mwanayo adayamba kulira.
17
Mulungu adamumva mwanayo akulira, ndipo mngelo wa Mulungu adalankhula ndi Hagara kuchokera kumwamba, adati, “Kodi iwe Hagara, chikukuvuta nchiyani? Usachite mantha. Mulungu wamva kulira kwa mwanayu.
18
Dzuka, pita, ukamnyamule ndi kumgwiritsa ndi dzanja lako. Zidzukulu zako zidzakhala mtundu waukulu.”
19
Apo Mulungu adatsekula maso a Hagara, ndipo adaona chitsime. Iye adapita pachitsimepo, nakadzaza thumba lachikopa lija ndi madzi, nkumwetsako mwanayo.
20
Mulungu adakhala naye mwanayo mpaka kukula. Adakulira m'chipululu cha Perani, nasanduka katswiri wa uta.
21
Mai wakeyo adampezera mkazi wa ku Ejipito.
22
Pa nthaŵi imeneyo Abimeleki, pamodzi ndi Fikolo, mkulu wa gulu lake la ankhondo, adapita kwa Abrahamu kukamuuza kuti, “Inu, Mulungu ali nanu pa zonse zimene mumachita.
23
Nchifukwa chake tsono, lumbirani pano pamaso pa Mulungu kuti simudzandinyenga ineyo, kapena ana anga, kapenanso zidzukulu zanga. Ine ndakhala wokhulupirika kwa inu, ndiye inunso mulonjeze kuti mudzakhala wokhulupirika kwa ine, m'dziko limene mukukhalamolo.”
24
Abrahamu adati, “Ndikulumbira.”
25
Pambuyo pake Abrahamu adamdandaulira Abimeleki za chitsime chimene antchito ake adaalanda.
26
Abimeleki adati, “Sindikudziŵa amene adachita zimenezi. Ngakhale inu nomwe simudandiwuze, ndipo ine kumva nkomweku.”
27
Abrahamu adapatsa Abimeleki nkhosa ndi ng'ombe, ndipo onse aŵiriwo adachita chipangano.
28
Abrahamu adapatulako anaankhosa asanu ndi aŵiri kuchotsa pa zoŵeta zake.
29
Abimeleki adamufunsa kuti “Chifukwa chiyani mukuchita zimenezi?”
30
Abrahamu adayankha kuti, “Inu landirani nkhosa zisanu ndi ziŵirizi, chifukwa mukatero mukuvomereza kuti chitsimechi ndidakumba ndine.”
31
Motero malo amenewo adatchedwa Beereseba chifukwa kumeneko ndiko kumene anthu aŵiriwo adachita chipangano.
32
Atachita chipangano chimenechi ku Beereseba kuja, Abimeleki ndi Fikolo mkulu wa gulu la ankhondo, adabwerera kwao ku dziko la Afilisti.
33
Tsono Abrahamu adabzala mtengo wa mbwemba ku Beereseba, natama dzina la Chauta, Mulungu Wamuyaya, mopemba.
34
Ndipo adakhala m'dziko la Afilisti nthaŵi yaitali.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50