bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 49
Genesis 49
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 48
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 50 →
1
Pambuyo pake Yakobe adaitana ana ake naŵauza kuti, “Sonkhanani pamodzi, kuti ndikuuzeni zimene zidzakuchitikireni m'tsogolo muno.
2
“Bwerani kuno, ndipo mumve, inu ana a Yakobe, mverani bambo wanu Israele.
3
“Rubeni mwana wanga wachisamba, ndiwe nkhongono zanga, ndiwe mphatso yoyamba ya mphamvu zanga. Mwa ana anga onse, wopambana ndiwe pa ulemerero ndi mphamvu.
4
Uli ngati chigumula cha madzi oopsa, koma sudzakhalanso wopambana, chifukwa chakuti sudaope kugona pa bedi la ine bambo wako. Udaloŵa m'bedi langa, nuliipitsa!
5
“Simeoni ndi Levi mpachibale pao, amagwiritsa ntchito zida zankhondo pochita chiwawa.
6
Ine sindidzakhala nao pa zokambirana zao zam'seri, sindifuna kukhala nao m'misonkhano yao, chifukwa choti adapha anthu mokalipa, ndipo adapundula ng'ombe zamphongo mwankhanza, naziyesa choseketsa.
7
Matemberero aŵagwere, chifukwa mkwiyo wao ndi woopsa kwambiri, ukali wao utembereredwenso, chifukwa imeneyo ndi nkhalwe. Ndidzaŵamwaza iwowo m'dziko lonse la Yakobe. Ndidzaŵabalalitsa pakati pa Israele.
8
“Iwe Yuda, abale ako adzakutamanda. Adani ako udzaŵagwira pa khosi, abale ako adzakugwadira iwe.
9
Yuda ali ngati msona wa mkango. Ukapha, umabwereranso kumalo kumene umabisala. Yuda ali ngati mkango, amatambasuka nagona pansi. Iye ndi mkangodi, ndipo palibe amene angalimbe mtima kuti amdzutse.
10
Ndodo yaufumu siidzachoka mwa Yuda, adzachita kuupanira ufumu umenewo, adzasunga mphamvu zake, mpaka mwiniwake weniweni atabwera, wodzalamulira anthu onse.
11
Bulu wake amamumangirira ku mtengo wamphesa, mwanawabulu ku mpesa wabwino. Zovala zake amazichapa mu vinyo, mu vinyo wofiira ngati magazi.
12
Maso ake ndi ofiira ndi vinyo mano ake ndi oyera ndi mkaka.
13
“Zebuloni adzakhala m'mbali mwa nyanja, madooko ake adzakhala malo a zombo, dziko lake lidzafika mpaka ku Sidoni.
14
“Isakara ali ngati bulu wamphamvu, amagona chotambasuka pakati pa makola.
15
Ataona kukoma kwa malo ousirapowo, ndi kukongola kwa dzikolo. Adaŵeramitsa msana kuti anyamule katundu wake, ndipo adasanduka womagwira ntchito yaukapolo.
16
“Dani adzalamulira anthu ake. Anthuwo adzalingana ndi mafuko ena a Israele.
17
Dani adzakhala ngati njoka pambali pa mseu, njoka yaululu ndithu m'mbali mwa njira, yoluma ku chidendene cha kavalo, kotero kuti wokwerapo wake adzagwa chagada.
18
“Ndikuyembekeza chipulumutso chanu, Inu Chauta.
19
“Gadi anthu achifwamba adzamthira nkhondo, koma iyeyo adzaŵatembenukira nkuŵapirikitsa.
20
“Dziko la Asere lidzabala chakudya chokoma, choyenera kudya mafumu.
21
“Nafutali ali ngati insa yongoyenda mwaufulu, imene imabala ana okongola.
22
“Yosefe ali ngati nthambi yobala zipatso, nthambi yobala zipatso pafupi ndi kasupe, nthambi yotambasuka pa khoma.
23
Adani ake adalimbana naye mwankhalwe, namthamangitsa ndi mauta ao.
24
Koma iyeyo uta wake sudagwedezeke, mikono yake idalimbika, ndi mphamvu za Mulungu Wamphamvuzonse wa Yakobe, amene ali Mbusa ndi Thanthwe la Israele.
25
Ndi Mulungu wa atate ako amene amakuthandiza, ndi Mulungu Mphambe amene amakudalitsa. Amakudalitsa ndi mvula yochokera mu mlengalenga, ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka, ndipo adzakudalitsa pakukupatsa ana ambiri ndi ng'ombe zambiri.
26
Madalitso a bambo wako ndi amphamvu kupambana madalitso a mapiri amuyaya, kupambananso zabwino za ku zitunda zamuyaya. Zimenezi zidzakhala pamutu pa Yosefe, pamphumi pa kalonga amene adampatula pakati pa abale ake.
27
“Benjamini ali ngati mmbulu wolusa umene m'maŵa umapha ndi kudya zimene udagwira, ndipo madzulo umagaŵa zimene udagwirazo.”
28
Aŵa ndiwo akulu a mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele, ndipo zimenezi nzimene bambo wao Yakobe adaŵauza, pamene ankadalitsa aliyense mwa iwo potsazikana nawo.
29
Tsono Yakobe adaŵalamula ana akewo kuti, “Popeza kuti tsopano ndilikufa, mukandiike m'phanga limene lili m'munda wa Efuroni Muhiti, ku Makipera.
30
Lili kuvuma kwa Mamure m'dziko la Kanani. Abrahamu adaagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efuroni Muhiti, kuti pakhale manda.
31
Kumeneko ndiko kumene adaika Abrahamu pamodzi ndi Sara mkazi wake. Isaki pamodzi ndi mkazi wake Rebeka, adaŵaikanso komweko, ndipo Leya ndidamuika komwekonso.
32
Mundawo pamodzi ndi phangalo adagula kwa Ahiti.”
33
Tsono Yakobe atamaliza kulangiza ana ake, adabwezeranso mapazi ake m'bedi ndipo adamwalira.
← Chapter 48
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 50 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50