bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 36
Genesis 36
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 37 →
1
Nazi zidzukulu za Esau, amene ankatchedwanso Edomu.
2
Esau adaakwatira akazi Achikanani aŵa: Ada mwana wa Eloni Muhiti, Oholibama mwana wa Ana, mwana wa Zibiyoni Muhivi,
3
ndi Basemati mwana wa Ismaele, mlongo wa Nebayoti.
4
Ada adamubalira Esau Elifazi. Basemati adabala Reuele
5
ndipo Oholibama adabala Yeusi, Yalamu ndi Kora. Ameneŵa ndi ana amene adabereka Esau m'dziko la Kanani.
6
Tsono Esau adatenga akazi ake, ana ake aamuna, ana ake aakazi ndi anthu onse a m'nyumba mwake, pamodzi ndi zoŵeta zake zonse, ndi katundu wake yense amene adampeza ku dziko la Kanani, ndipo adasiyana ndi mbale wake uja Yakobe, napita kukakhala ku dziko lina.
7
Chimene adachokera ndi chakuti dziko limene ankakhalako iye pamodzi ndi Yakobe, silinkaŵakwanira aŵiriwo. Anali ndi zoŵeta zochuluka zedi, mwakuti sikudatheke kuti iwo akhale pa malo amodzi.
8
Motero Esau adakakhala m'dziko lamapiri ku Edomu.
9
Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu, okhala m'dziko lamapiri la Seiri.
10
Maina a ana aamuna a Esau naŵa: Elifazi mwana wa Ada mkazi wa Esau, ndi Reuele mwana wa Basemati mkazi wa Esau.
11
Ana a Elifazi ndi Temani, Omara, Zefo, Gatamu ndi Kenazi.
12
(Timna anali mzikazi wa Elifazi mwana wa Esau, ndipo mwa Timnayo Elifazi adaberekamo Amaleke.) Ameneŵa ndiwo ana a Ada mkazi wa Esau.
13
Ana a Reuele ndi aŵa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Ameneŵa ndiwo ana a Basemati mkazi wa Esau.
14
Ana a Oholibama mkazi wa Esau ndi aŵa: Yeusi, Yalamu ndi Kora. Oholibamayo anali mwana wa Ana mwana wa Zibiyoni.
15
Naŵa mafumu a zidzukulu za Esau. Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau, panali mafumu aŵa: Temani, Omara, Zefo, Kenazi,
16
Gatamu ndi Amaleke. Ameneŵa ndi mafumu mwa ana a Elifazi m'dziko la Edomu. Onseŵa anali ana a Ada.
17
Mwa ana a Reuele, mwana wa Esau, panali mafumu aŵa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Ameneŵa ndiwo mafumu mwa ana a Ruwele m'dziko la Edomu, ndiponso ndiwo ana a Basemati mkazi wa Esau.
18
Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau, panali mafumu aŵa: Yeusi, Yalamu ndi Kora. Ameneŵa ndiwo mafumu amene mkazi wa Esau, Oholibama mwana wa Ana, adabala.
19
Ameneŵa ndi zidzukulu zake za Esau, ndiponso ndiwo mafumu ao.
20
Aŵa ndi ana aamuna a Seiri Muhori, nzika za dzikolo: Lotani, Sobali, Zibiyoni ndi Ana,
21
Disoni, Ezere ndi Disani. Aŵa ndiwo mafumu a Ahori ana a Seiri m'dziko la Edomu.
22
Ana a Lotani anali Hori ndi Hemani, ndipo Timna anali mlongo wa Lotani.
23
Ana a Sobali ndi aŵa: Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.
24
Ana a Zibiyoni ndi aŵa: Aya ndi Ana. (Ameneyu ndiye Ana amene adapeza akasupe otentha m'chipululu, pamene ankadyetsa abulu a Zibiyoni bambo wake.)
25
Ana a Ana ndi aŵa: Disoni mwana wake wamwamuna, ndi Oholibama mwana wake wamkazi,
26
Ana aamuna a Disoni ndi aŵa: Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani.
27
Ana a Ezere ndi aŵa: Bilihani, Zaavani ndi Akani.
28
Ana a Disani ndi aŵa: Uzi ndi Arani.
29
Mafumu a Ahori ndi aŵa: Lotani, Sobali, Zibiyoni, Ana,
30
Disoni, Ezere ndi Disani. Ameneŵa ndiwo mafumu a Ahori m'dziko la Seiri malinga ndi mafuko ao.
31
Naŵa mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mafumu a Aisraele asanayambe kulamulira kumeneko:
32
Bela mwana wa Beori, ankalamulira dziko la Edomu, ndipo dzina la mzinda wake linali Dinihaba.
33
Bela atafa, Yobabu mwana wa Zera wa ku Bozira ndiye amene adaloŵa ufumu m'malo mwake.
34
Yobabu atafa, Husamu wa ku dziko la Atemani adaloŵa ufumu m'malo mwake.
35
Atafa Husamu, Hadadi mwana wa Bedadi adaloŵa ufumu m'malo mwake. Iyeyu ndiye amene adagonjetsa Amidiyani m'dziko la Mowabu, ndipo dzina la mzinda wake linali Aviti.
36
Atafa Hadadi, Samila wa ku Masireka ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake.
37
Atafa Samila, Shaulo wa ku Rehoboti, mzinda wa pa mtsinje wa Yufurate, ndiye amene adaloŵa ufumu m'malo mwake.
38
Atafa Shaulo, Baala-Hanani mwana wa Akibori, ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake.
39
Baala-Hanani mwana wa Akibori atafa, Hadari ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake. Dzina la mzinda wake linali Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehetabele, mwana wa Matiredi mwana wa Mezahabu.
40
Aŵa ndiwo mafumu a kubanja kwa Esau mwatsatanetsatane, malinga ndi mafuko ao ndi malo a fuko lililonse: Timna, Aliva, Yeteti,
41
Oholibama, Ela, Pinoni,
42
Kenazi, Temani Mibizara,
43
Magadiele ndi Iramu. Ameneŵa ndiwo mafumu a Edomu (ndiye kuti Esau kholo la Aedomu potsatana ndi malo omwe ankakhala m'dziko laolo.)
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 37 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50