bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Genesis 24
Genesis 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 25 →
1
Tsopano Abrahamu anali atakalamba, atagonera zaka zochuluka, ndipo Mulungu adaamudalitsa pa zonse zimene ankachita.
2
Tsiku lina adauza wantchito wake wamkulu amene ankayang'anira zinthu zake zonse kuti, “Tandigwira m'kati mwa ntchafu zangamu.
3
Ndikufuna kuti ulumbire pamaso pa Chauta, Mulungu wa dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, kuti sudzamufunira mbeta mwana wanga pakati pa atsikana Achikanani kuno ndili ine kuno.
4
Koma udzapita ku dziko lakwathu, ndipo ukamutengera mkazi mwana wanga kumeneko pakati pa abale anga.”
5
Koma wantchitoyo adafunsa kuti, “Nanga zidzatani mkaziyo akadzakana kubwera nane kuno? Kodi mwana wanuyo ndidzamperekeze ku dziko lanu kumene mudachokera?”
6
Abrahamu adayankha kuti, “Usadzamperekeze kumeneko mwana wangayo.
7
Chauta, Mulungu Wakumwamba, adanditenga kwathu m'banja mwa bambo wanga ndi m'dziko limene ndidabadwira, ndipo adandilonjeza molumbira kuti, ‘Dziko lino ndidzapatsa zidzukulu zako.’ Chautayo adzatuma mngelo wake wokutsogolera, ndipo kumeneko udzamutengera mkazi mwana wanga.
8
Koma ngati mkaziyo adzakana kubwera nawe kuno, udzamasuka ku lumbiro limeneli. Komabe mwa njira iliyonse, mwana wanga usadzapite naye kuti akakhale kumeneko.”
9
Motero wantchitoyo adaika dzanja lake m'kati mwa ntchafu za Abrahamu mbuye wake, ndipo adalumbira kuti, “Ndidzachita zonse zimene mwanenazi.”
10
Tsono wantchitoyo adatenga ngamira khumi za mbuye wake, ndi mphatso zambiri zamtengowapatali, ndipo adapita ku mzinda wa Nahori, m'dziko la Mesopotamiya.
11
Atafika, adazigwaditsa pansi ngamirazo pafupi ndi chitsime, kunja kwa mzinda. Anali madzulo ndithu, nthaŵi imene akazi ankabwera kuchitsimeko kudzatunga madzi.
12
Ndipo wantchito uja adayamba kupemphera, adati, “Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ndikukupemphani kuti zinthu zitheke lero lino, ndipo muwonetse chikondi chanu chosasinthika chimene muli nacho pa mbuyanga Abrahamu.
13
Ndili pano pa chitsime, ndipo akazi amumzindamu abwera kudzatunga madzi.
14
Ine ndipempha namwali wina kuti, ‘Chonde tatsitsa mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono namwaliyo akandilola kuti, ‘Imwani, ndipo ndikumwetserani ngamira zanu,’ ameneyo ndiye akhale namwali amene mwasankhira mtumiki wanu Isaki. Zimenezi zikachitika, ndidziŵadi kuti mwamkomera mtima mbuyanga.”
15
Asanamalize nkomwe kupemphera, anangoona uyu, watulukira Rebeka, atasenza mtsuko pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betuele, mwana wa Milika, mkazi wa Nahori, mbale wake wa Abrahamu.
16
Anali namwali wosadziŵa mwamuna aliyense, wokongola kwambiri. Iye adatsikira kuchitsime kuja, natunga madzi mu mtsuko, nkutulukako.
17
Tsono wantchito uja adamthamangira kuti akakumane naye, nampempha kuti, “Chonde mundipatseko madzi a mumtsuko mwanu kuti ndimwe.”
18
Namwaliyo adati, “Imwani mbuyanga,” ndipo mosachedwa adatsitsa mtsuko wake uja pa phewa, naugwirira kuti mlendoyo amwe.
19
Mlendo uja atamwa madziwo, namwaliyo adati, “Ndibwera nawonso madzi, kuti zimwe ngamira zanu mpaka zikwane.”
20
Pompo madzi amumtsukowo adaŵatsanyulira m'chomwera nyama, nabwerera ku chitsime kukatenga madzi ena oti amwetse ngamirazo mpaka zitakwana.
21
Munthu uja anali phee, kuyang'ana zimene ankachita namwaliyo, kuti aone ngati Chauta wadalitsa ulendo wake kapena ai.
22
Namwali uja atamaliza kumwetsa ngamirazo, munthuyo adatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli, naveka Rebeka pamphuno pake. Adamuvekanso pamikono pake zigwinjiri ziŵiri zolemera masekeli agolide okwana 100.
23
Kenaka adafunsa namwaliyo kuti, “Kodi atate anu ndani? Tandiwuzani chonde. Kodi alipo malo oti ine ndi anzangaŵa nkugonako usiku uno?” Namwaliyo adayankha kuti,
24
“Ine ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori, amene adamubalira Milika.” Adapitiriranso kunena kuti,
25
“Chakudya chodyetsa nyamazi chiliko kwathu, ndipo malo oti inu mugoneko aliponso.”
26
Pamenepo munthu uja adaŵerama nkupembedza Chauta,
27
ndipo adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene wasunga mokhulupirika lonjezo lake kwa mbuyanga. Chauta wandilondolera ine ku nyumba ya mbale wake wa mbuyanga.”
28
Tsono namwali uja adathamangira kunyumba kwa mai wake, nafotokozera onse nkhani yonseyo.
29
Apo Labani, mlongo wa Rebekayo, adaonadi chipini chija pamodzi ndi zigwinjiri pa mikono ya mlongo wakeyo.
30
Atamva mlongo wake akusimba zimene munthu uja adaamuuza, Labaniyo adathamangira kuchitsime kumene kunali munthuko. Adakafika pamalo pomwe adaaima wantchito wa Abrahamu, pafupi ndi ngamira zija kuchitsimeko.
31
Adauza munthuyo kuti, “Tiyeni kwathu, inu ndinu munthu amene Chauta wakudalitsani. Bwanji mukuima kuno? Ine ndakukonzerani kale malo kunyumba, ndiponso malo a ngamira zanu.”
32
Motero munthu uja adakaloŵa m'nyumba, ndipo Labani adamasula katundu amene zidaasenza ngamirazo. Atatero adazipatsa chakudya, naŵapatsa madzi alendo onsewo kuti asambe.
33
Chitabwera chakudya, munthu uja adati, “Sindidya konse mpaka nditanena zimene ndadzera.” Apo Labani adamuuza kuti, “Nenani.”
34
Iyeyo adati, “Ine ndine wantchito wa Abrahamu.
35
Chauta adamdalitsa kwambiri mbuyanga, ndipo adamkuza kwambiri. Ali ndi nkhosa ndi mbuzi ndi ng'ombe zochuluka. Alinso ndi siliva ndi golide, akapolo aamuna ndi aakazi, ndiponso ngamira ndi abulu ambiri.
36
Sara, mkazi wake wa mbuyanga, adamubalira mwana wamwamuna, Sarayo atakalamba kale. Ndipo mbuyangayo wamupatsa chuma chake chonse mwana ameneyo.
37
Tsono mbuyanga adandilumbiritsa kuti ndisunge mau ake akuti, ‘Mwana wangayu usadzamfunire mbeta pakati pa anamwali a dziko lino la Kanani, kumene ndili ine kuno.
38
Koma upite kwathu kwa atate anga ndi achibale anga, kukamutengera mkazi mwana wanga kumeneko.’
39
Ndipo ine ndidamuyankha mbuyanga kuti, ‘Nanga zidzatani ngati mkaziyo adzakana kubwera nane kuno?’
40
Iye adandiyankha kuti, ‘Chauta amene ndakhala ndikumumvera nthaŵi zonse, adzatuma mngelo wake kuti apite pamodzi nawe, ndipo adzakuthandiza. Udzampezera mkazi mwana wanga pakati pa anthu anga, m'banja la bambo wanga.
41
Ukachita zimenezi, matemberero anga sadzakugwera. Koma iweyo utafika ku banja langalo, anthu angawo nakakukana, udzamasuka ku lumbiro lako.’
42
“Tsono lero lino nditafika ku chitsime, ndinapemphera kuti, ‘Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, chonde mundithandize kuti ndikhoze pa ulendo wangawu.
43
Ndili pano pachitsime, pakabwera namwali pano kudzatunga madzi, ine ndidzampempha kuti: Chonde patseko madzi a mumtsuko mwako kuti ndimwe.
44
Iye akandiyankha kuti: Imwani ndipo ndimwetsanso ngamira zanuzi, ameneyo ndiye akhale namwali amene Chauta wamsankha kuti akhale mkazi wa mwana wa mbuyanga.’
45
Ndisanamalize nkomwe pemphero langalo, ndinangoona uyu, watulukira Rebeka, atasenza mtsuko pa phewa, akutsikira ku chitsime kudzatunga madzi. Tsono ndinampempha kuti, ‘Chonde patseko madzi ndimwe.’
46
Mosachedwa anatsitsa mtsuko wake pa phewa, nandiwuza kuti, ‘Imwani, ndipo ndimwetsanso ngamira zanuzi.’ Motero ine ndinamwa, ndipo iye anamwetsanso ngamirazo.
47
Ndiye ndinamufunsa kuti, ‘Atate ako ndani?’ Iye anandiyankha kuti, ‘Atate anga ndi Betuele, mwana wa Nahori, amene adamubalira Milika.’ Pamenepo ndinamuveka chipini pa mphuno, ndiponso zigwinjiri pa mikono.
48
Kenaka ndinaŵerama, nkupembedza Chauta. Ndinatamanda Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, chifukwa cha kunditsogolera bwino kwambiri. Chauta wandifikitsa kwa mbale wake wa mbuyanga, kumene ndapezako mwana wake amene adzakhale mkazi wa mwana wa mbuyanga.
49
Tsopano inu ngati muti mumkomere mtima mbuyanga mokhulupirika, chonde uzeni ndimve. Apo ai, nenaninso, kuti ine ndidziŵe chochita.”
50
Pamenepo Labani ndi Betuele adauza munthuyo kuti, “Popeza kuti zimenezi nzochokera kwa Chauta, ife sitingachitepo kanthu.
51
Nayu, Rebeka ndi ameneyu, mtengeni muzipita naye. Mukampereke kwa mwana wa mbuyanuyo kuti akakhale mkazi wake, monga momwe Chauta adanenera.”
52
Wantchito wa Abrahamu uja atamva mau ao aja, adaŵeramitsa mutu napembedza Chauta.
53
Kenaka adatulutsa zinthu zasiliva ndi zagolide, pamodzi ndi zovala, napatsa Rebeka. Adaperekanso mphatso zamtengowapatali kwa mlongo wake wa Rebekayo ndi kwa mai wake.
54
Wantchitoyo pamodzi ndi anthu amene anali nayewo adadya ndi kumwa, ndipo adagona komweko. Atadzuka m'maŵa, mlendoyo adati, “Loleni ndizibwerera kwa mbuyanga.”
55
Koma mai wake wa Rebeka, pamodzi ndi mlongo wakeyo, adati, “Ai, namwaliyu akhale ndi ife kuno kanthaŵi, osachepera masiku khumi, pambuyo pake ndiye adzapite.”
56
Koma wantchitoyo adati, “Chonde musandichedwetse. Chauta wandithandiza kwambiri pa ulendo wangawu. Loleni tsono ndibwerere kwa mbuyanga.”
57
Apo iwowo adayankha kuti, “Tiyeni timuitane namwaliyo, kuti timve zimene iyeyo anene.”
58
Motero adamuitana Rebeka namufunsa kuti, “Kodi ukufuna kupita naye munthuyu?” Rebekayo adayankha kuti, “Inde, ndipita.”
59
Choncho adamlola Rebeka pamodzi ndi mlezi wake, kuti apite ndi wantchito wa Abrahamu ndi anthu aja omuperekezaŵa.
60
Ndipo adamdalitsa Rebekayo ponena mau akuti, “Iwe mwana wathu, Chauta akudalitse kuti udzakhale mai wa anthu zikwi zambirimbiri. Zidzukulu zako zidzagonjetse mizinda ya adani ao.”
61
Pomwepo Rebeka pamodzi ndi atsikana ake antchito adanyamuka nakakwera ngamira, nkumapita ndi munthu uja.
62
Isaki anali atachoka kuchipululu kumene kunali chitsime cha Wamoyo-Wondipenya chija, kukakhala m'chigawo chakumwera.
63
Tsiku lina madzulo, Isakiyo ankapita nayenda kuthengo, ndipo adaona ngamira zilikudza.
64
Tsono Rebeka ataona Isaki, adatsika pa ngamira yake ija,
65
nafunsa wantchitoyo kuti, “Nanga munthu ali akudza kunoyu ndani?” Wantchito uja adayankha kuti, “Ndiye mbuyanga uja ameneyu.” Motero Rebeka adatenga nsalu, nadziphimba kumaso.
66
Wantchitoyo adamufotokozera Isaki zonse zimene zidaachitika.
67
Tsono Isaki adatenga Rebeka kuti akhale mkazi wake naloŵa naye m'hema mwake. Isaki adamkonda kwambiri Rebekayo, mwakuti zimenezi zidamtonthoza pa imfa ya mai wake ija.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50